Tobias auza Chakwera zina mwa njira zokonzera chuma

Yemwe akufuna kudzayima nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino, a Milward Tobias, wauza mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus McCarthy Chakwera, kuti afunsire nzeru kwa anthu ena pa mmene angathanirane ndi mavuto a zachuma omwe akuta dziko lino.

Tobias: Malawi ruled like a mafia

A Tobias, omwe ndi katswiri pa nkhani za chuma, ati mavuto a za chuma omwe aMalawi akukumana nawo pakali pano adachita kudzalidwa ndi utsogoleri wa boma la Tonse kudzera mu ndondomeko zoyendetsa chuma zolakwika, makamaka bajeti ya boma.

Choncho, a Tobias apempha Chakwera kuti aganizire mozama za kufunikira kofunsira nzeru kwa anthu ena pa mmene angakonzere zinthu, makamaka mmene angakonzere ndondomeko ya zachuma (bajeti) yomwe ingayankhe mavuto omwe aMalawi akukumana nawo.

Iwo anenetsa kuti bajeti ndi chida chimene chiri ndi kuthekera kokonza kapena kuononga chuma kutengera mmene bagetiyo ikuyendetsedwera.

Anapitiriza ponena kuti ndi zomvetsa chisoni kuti litangolowa m’boma mchaka cha 2020, atsogoleri a Tonse sadafune kumva malangizo a anthu ena pa mmene angayendetsere zinthu ndi cholinga choti chuma chiyambirenso kuyenda bwino.

“Atangolowa mu boma ndikupereka bajeti yoyamba ku Nyumba ya Malamulo, ndidayankhula ku wailesi ina kuti ayika poison mu chuma cha dziko dzitivuta kutsogolo. Chuma chimayenda ngati thanzi la munthu. Kachilombo koyambitsa matenda kangathe kulowa mthupi lero nkuyamba kudwala lero lomwe kapena patatha nthawi mwina zaka zimene kakuswana kenako nkudzadwala. Aliyense amene amadziwa bwino mmene chuma cha dziko chimayendera ndi mmene chuma cha Malawi chidasanjanirana, ndikukhulupirira sakudabwa kuti tafika pamenepa. Boma lawononga chumachi,” anatero Tobias pocheza ndi mtolankhaniyu.

Iwo ati ichi ndi chifukwa chake dziko la Malawi lili pa moto, ndipo pakufunika yankho la msangamsanga.

A Tobias atsindika kunena kuti udindo wopeza yankho uli mwa amene akutsogolera amene ndi president ndi timu yake, ponena kuti udindo wa ena ndiye ndi kungopereka maganizo kaamba kuti malamulo sakuwapatsa mphamvu yochita ziganizo zofunikira.

“Ndi zachisoni kwambiri kuti chuma cha dziko chaphwasuka. Chuma cha munthu ndi banja chaphwasuka. Ndalama yatha mphamvu chifukwa mitengo ya katundu ikukwera mowirikiza. Zimene timakwanitsa kugula ndi ndalama imene timayipeza sitikukwanitsanso. Umphawi, njala zafika ponyanya.

“Ndalama za kunja kulibe zimene zapha mabizinezi, zadzetsa kusowa kwa mankhwala ku chipatala komanso kusowa kwa mafuta a galimoto kuphatikiza kupangitsa kuti mitengo ya katundu ikhale yokwera mosafikirika kwa ogula. Chifukwa anthu sakugula, ochita malonda sakugulitsa, bizinezi yopanda kasitomala siyingayende. Ndalama za mdziko momwe muno zachepa kwambiri kufikira pakuti maunduna a boma ndi maboma ang’ono akulephera kugwira ntchito mmene akadagwirira. Anthu a bizinezi amene adaperekera katundu ku boma sakulipidwa. Ntchito za boma zotumikira nzika zake zaima,” anafotokoza motere iwowo.

A Tobias anapereka njira zikulu zikulu zinayi zomwe dziko limapezera ndalama za kunja. Njirazi ndi kugulitsa katundu ku misika ya kunja, thandizo lochokera ku maiko ndi mabungwe a kunja komanso ngongole za kunja, mabizinezi a kunja odzayambitsa ntchito za bizinezi mdziko muno komanso ndalama zotumiza kuno kuchokera kwa aMalawi amene ali kunja.

Iwo anati kwa zaka zambiri, ndalama zimene timapeza tikagulitsa katundu kunja (exports) zimakwana theka kapena gawo limodzi mwa magawo atatu a ndalama zimene zimafunika kuti tilipire katundu wa kunja (half or one-third of import bill).

“Timasokerera mbali yotsala ndi njira zina zitatuzo. Izi zakhala motere kwa nthawi yayitali. Ndi vuto lofunika kukonza koma chuma chikamayendetsedwa bwino sitilimva. Ndalama zotithandiza maiko ndi mabungwe a kunja ziri magawo awiri. Gawo limodzi ndi ndalama zimene amatipatsa kukhala mbali ya bajeti ndipo timakhala ndi ufulu kuzigwiritsa ntchito mbali imene tikufuna komanso nthawi imene tikufuna. Gawo lina ndi ndalama zobwera kuthandiza pulojeketi imene otithandizawo ndi ife tagwirizana. Ndalama izi zimakhala zotetezedwa kutero kuti pokhapokha ntchito ikugwirika ndi pamene dziko lathu limapeza ndalama za kunja zimenezo akamalipira anthu ndi katundu mu makwacha amakhala atasintha zakunjazo. Ngati ntchito ikuchedwa ndiye kuti ndalama zimenezo sizingagwiritsidwe ntchito. Izi ndikunena chifukwa a president a dziko lino nthawi ina ankadandaula kuti ma pulojeketi akuchedwa. Chimene mwina samadziwa nkuti anthu amene akuchedwetsawo amene iwo ali ndi mphamvu yowachotsa ntchito chifukwa adawaika okha, amatsekereza ndalama za kunja kupatula kuchedwetsa mwai wa ntchito kwa anthu komanso chitukuko,” anapitiriza kufotokoza motere.

Pakali pano, a Tobias alangiza President Chakwera kuti afikire anzawo ndi cholinga choti apeze nzeru zokonzera zinthu.

“Mr President, dziko lino liri pa moto. Tikufuna yankho lero osati mawa. Ndikuganiza njira izi:

1. Fikirani anzanu muwauze kuti dziko liri pa ngozi ndipo mukupempha thandizo lawo. Anzanu adapanga chaka cha 2012 mu nthawi yochepa ndalama za kunja zidapezeka. Inu mwakhala president zaka zinai, mwapanga ubwenzi ndi ma president anzanu. Afikireni.

2. Nduna yanu ya za chuma ifikire maiko ndi mabungwe amene akuthandiza ma pulojeketi osiyanasiyana ndikuwapempha atipatse ndalama za pulojeketi zo kweni kweni gawo limene adzalipira anthu ndi katundu mu ndalama yathu ya kwacha. Boma lidzibweza pang’ono pang’ono molingana ndi ndalama zofunika kulipira pa nthawi ndi ntchito imene yagwirika kuti pulojeketi idziyenda.

3. Funani ngongole ya kunja imene chiwongola dzanja ndichotsika komanso itibweretsera ndalama za kunja mwansanga

4. Konzani bajeti ya 2025-2026 mochepetsa kulekana kwa ndalama zimene mukuyembekeza kupeza ndi ndalama zofunika kugwiritsa ntchito kuti potero muyambe kubwezeretsa chuma mchimake. Mukatero chiwongola dzanja chiyamba katsika. Mabanki ndi ena obwereketsa ndalama akhala ndi ndalama zimene adzisaka woti abwereke potero afewetsa zimene amafuna kwa obwereka mpamba. Pakadali pano boma likumasesa ndalama zonse zimene a bizinezi akanabwereka zimene zathandizira kupha mabizinezi komanso kupha chuma cha dziko.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter