Amalawi ayamba kukolola zipatso za ulendo wa Chakwera ku Belgium

Amalawi ayamba kukolola zipatso za ulendo wa mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus McCarthy Chakwera, ku dziko la Belgium mchaka cha 2022 pamene makampani a ku dziko la Belgium tsopano ayamba kugwira ntchito zawo mdziko muno.

Imodzi mwa makampani omwe Chakwera adakakumana nawo ku Belgium ndi Phillip Morris yomwe Lachinayi yatsimikizira Amalawi za kudzipereka kwake pa kugwira ntchito ndi boma la Malawi pokhazikitsa pulogramu othandiza alimi kupeza mwayi obwereka makina aulimi.

Polankhula pa mwambo wokhazikitsa ntchito zotukula ulimi podzera mkugwiritsa ntchito makina womwe unachitikira ku Bingu International Convention Centre ku Lilongwe, a Chakwera anatsindika za kufunikira za kogwira ntchito ndi makampani akunja ngati Phillip Morris potukula ulimi.

“Kampani imeneyi nditakumana nayo inandiuza kuti ndisanabwelere kuno ku Malawi ndipite ku ofesi yawo yaikulu yomwe iri ku Switzerland, ndiye kutereku ananditenga kuchoka ku Belgium mpaka kukafika kumeneko, ndicholinga choti tikakhale pansi nkukambirana za mmene iwo angathandizire dziko lathu kuchita ulimi wamakono komanso minda ikuluikulu ija tikumati Mega Farm. Ndiye titamaliza kumeneko ndinawauza aunduna wazaulimi kuti ndiwo zomwe ndinakatereka ku ulendo umenewo azilondole mpaka ziphye kuti aMalawi adzadye zipatso zake,” anatero mtsogoleriyu.

Chakwera anathokoza kampani ya Philip Morris kaamba komva pempo la mtsogoleri wadziko linoyu komanso pogwira ntchito mosalekeza zaka ziwiri zapitazi kuonetsetsa kuti izizi zitheke.

“Mwinanso ndinene pano kuti anthuwa nditakumana nawo ndinawauza kuti ifeyo monga a Malawi masomphenya athu a Malawi 2063 ndikuchulikitsa chuma chathu ndicholinga choti tikhale anthu odzidalira tokha, ndiye ndinanenelatu nthawi imeneyo kuti ife sitikufuna kupatsidwa zinthu zaulele. Tikufuna abale omwe angatipatse kuthekela kodzithandiza tokha chifukwa zaulele sizimathandiza kuti tikhale odzidalira tokha. Ndiye china chomwe chandisangalatsa lero ndichokuti awa a Philip Morris apereka chitsanzo chabwino polimbikitsa ulimi odzidalira tokha, chifukwa iwowa apeza kampane inzawo yakuno ku Malawi nkugwirana nayo manja kuti agwire ntchito limodzi powapatsa alimi mMalawi muno kuthekela kopeza makina apangira ulimi wa ma Mega Farm,” anatero Chakwera.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anapempha alimi omwe ali ndi mwayi wobwereka makinawa kuti awasamale komanso kubweza ngongole ndi cholinga choti pulogalamuyi ipindulire ambiri.

“Pulogramu takonzayi ndiyoti mukabwereka inu makinawa, pozabweza ngongoleyo ndalamayo tizaonjezera makina ena kuti mlimi nzanu nayenso azabwerekeko. Komanso inu aunduna wazaulimi musazilekelere zinthuzi, muzilondole kuti muonetsetse kuti makina onse agwiritsidwe ntchito mosamala komanso mobweretsa phindu mdziko mwathu,” iwo anafotokoza motero.

Pa nkhani ya chitukuko, a Chakwera anati chilowereni m’boma mmwezi wa Juni chaka cha 2020, boma lawo lakhala likuika maziko osiyanasiyana komanso kufetsa mbeu madera osiyanasiyana kuti mtsogolomu, Amalawi adzakolole chuma chochuluka.

Choncho, iwo anapempha Amalawi kuti alimbe mtima ponena kuti nthawi yomanga maziko ndi kufetsa imakhala nthawi ya msozi.

“Sikuti ndiye wina apezerepo mwayi otigwetsa mphwayi kumazaanamiza a Malawi kuti akanakhala iwowo m’boma bwezi tikumanga maziko osamva kuwawa. Limenelo ndibodza. Sizoona kuti lero wina wakhutakhuka nsima yogulira ndalama zomwe chipani chake chinaba m’boma m’mbuyomo, ndiye aziima pachulu nkumabwebweta kuti anakakhala m’boma a Malawi saanakamva ululu wa Covid, kapena ululu wakukwera mitengo kwa zinthu dziko lonse lapansi chifukwa cha nkhondo ya ku mmawa kwa Europe, kapena ululu wa Cyclone Ana ndi Gombe, kapena ululu wa Cyclone Freddy, kapena ululu wa El Nino, kapena ululu wadzingongole zakatapila zomwe iwo anazishosha m’mbuyomo, kapena ululu omwe a Malawi akhala akuumva chifukwa cha mayiko amene anasiya kutithandiza chifukwa cha umbava omwe unkachitika ine ndisanabwere. Kuyankhula koteroko ndikwantopola.

“Iwowo anathira poyizoni muufa ndiye mdziko muno mwakhala muli maliro aakulu, ndiye ife a Malawi atikhulupilira kuti tiyendetse mwambo wamalirowa molongosoka komanso tiatsogolere mpaka azapezenso chisangalalo ngati chomwe chikuchitika lerochi. Ndiye ndizomveka kuti munthu amene anathira poyizoni muufa uja abwere pano azizanena kuti panakakhala iyeyo bwenzi mulibe maliro mdziko muno? Anthu amenewa asatiyankhulitse pambali. Tiyeni tipitirize ulendo wathu okonza dzikoli chifukwa wina afune asafune, zomwe tachita lerozi sitisiya mpaka aMalawi onse aone phindu lake,” anatsindika a Chakwera.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter