Anthu achialubino adandaula kuti akumaphedwa kwambiri nthawi yachisankho ikayandikira
ABungwe la achialubino la Association of People Living with Albinism in Malawi (Apam) lati likuda nkhawa ndi chisankho chikubwerachi chifukwa ndi nthawi yomwe amachitiridwa nkhanza kapena kuphedwa kumene.

Mkulu wa bungweli a Young Muhamba ndiwo adandaula izi poyankhapo pa nkhani ya manda a munthu wachialubino omwe anafukulidwa ku Mulanje.
Apolisi m’boma la Mulanje akufunafuna anthu womwe anafukula manda a munthu wachialubinoyu.
Malingana ndi mneneri wapolisi m’bomalo a Innocent Moses, izi zinachitika m’mudzi mwa Chinomba ku dera la mfumu Chikumbu.
A Muhamba anati palibe chodabwitsa pa nkhaniyi, makamaka nthawi ya chisankho ikamayandikira.
“Nkhawa yanga ndiyoti nkhani za kuvulaza, kupha kapena kufukula manda a anthu achialubino sizikutha m’dziko muno. Nthawi zambiri apolisi akhala akuchita zinthu mochedwa, makamaka pa nkhani yomanga anthu ankhanzawa.
“Tikuwapempha kuti afufuze nkhaniyi ndi kumanga omwe akuchita izi. Pali chizolowezi choti zisankho zikayandikira, khalidwe lochitira nkhanza anthu achialubino likumakula. Kodi tilowera kuti?” Iwo anadandaula.
Mfumu Chikumbu inati inadandaula kwambiri itamva zoti m’dera lawo mwachitika zimenezo zomwe inati zikumachitika ndi anthu osakonda anzawo komanso opanda umunthu.
Mfumuyi inapemphanso apolisi kuti afufuze mwachangu nkhaniyo kuti omwe achita izi agwidwe.
A Moses anati apolisi m’bomalo ali pa kalikiliki kusaka achiwembuwo. Iwo anapempha anthu kuti azikanena kupolisi ngati akuganizira anthu ena.
Pa nkhani ya chitetezo cha anthu achialubino, mneneri wapolisi m’dziko muno a Peter Kalaya anati mavuto omwe anthu achialubino akukumana nawo akuwadziwa bwino.
“Choncho tikuwatsimikizira kuti tichita chilichonse chotheka kuteteza miyoyo m’mutu chimene chinachititsa kuti amwalire.
Follow and Subscribe Nyasa TV :