Boma lapanga phindu lokwana K36Bn kudzera ku ma kampani ake

Makampane aboma lomwe mtsogoleri wake ndi a Dr Lazarus McCarthy Chakwera apereka ku boma ndalama zokwana zokwana zokwana K36Billion.

Ndalama izi zaperekedwa ngati mbali imodzi ya phindu zomwe makampaniwa apanga.

Malingana ndi malipoti omwe adaperekedwa ku msonkhano omwe boma ndi makampanewa amasainilana ku BICC, ena mwa makampane omwe akupanga phindu ndipo akupereka ku boma ndi monga Tobacco Commission (TC), Malawi Gaming Board (MAGLA), Lilongwe Water Board (LWB), Electricity Generation Company (EGENCO).

Ndipo kampane ina yomwe ikuchita bwino ndi Electricity Supply Corporation of Malawi (ESCOM).

Mukulankhula kwawo, nduya ya zachuma a Simplex Chithyola Banda adati, chisinsi chagona ponena kuti ma kampane apatsidwe zofunika ndi cholinga chakuti agwire ntchito mosanyinyirika.

Iwo adati pali ma kampane wena omwe amafuna kugula dzimagalimoto dzodula pomwe sapanga phindu, “Ayi tele ndiye boma lake silimeneli”.

Naye yemwe amayang’anira ma kampani aboma a Peter Simbani anenetsa kuti izi zipitilira kamba kakuti ambiri mwa otsogolera ma kampaniwa ndi anthu omwe akugwira ntchito modzipereka ndinso mwaukadaulo.

Izi zikusiyana ndi nthawi ya m’mbuyo pomwe makampani aboma amakhala opereka ndalama ku zipani nkumapangira ma kampeni andale. Izi sizikuchitika mboma lomwe lilipo pano.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Subscribe
Notify of
guest

0 Comments
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
0
Would love your thoughts, please comment.x
()
x
Read previous post:
Kayelekera’s $200M comeback: Malawi bets big on Nuclear Energy

Malawi’s dormant Kayelekera Uranium Mine is powering back to life with a MK350 billion (US$200 million) investment from Australian firm...

Close