“Tipeleke Mwayi wina kwa Mai Banda kuti umoyo wa anthu usinthe” – Atero a Mwandira
Chipani cha Peoples(PP) chamemeza anthu kuti adzavotele mtsogoleri wawo Mai Joyce Banda yemwe adalamulira dzikoli kwa zaka ziwiri zokha kuti tsopano adzapitilize ntchito zake za chitukuko maka pa nkhani ya kupeleka mwayi kwa anthu kuchita ulimi wa ziweto ndi bizinesi za mayendedwe.
Gavanala wa chipanichi Ku dera la Mbayani ,Chemusa Magasa mu mzindawu Watson Mwandira ndiye wayankhula izi pamsokhano wokonzekeletsa anthu za kubwera kwa mtsogoleri wa chipanichi loweluka likudzali yemwe akuyembezereka kudzacheleza anthu Ku Ndirande pa bwalo la za masewelo la Nyambadwe.
Iye wati mu mbiri ya dziko lino ,Mai Joyce Banda ndi mtsogoleri yemwe anayambitsa Kabaza wa njinga (zamoto ndi za kapalasa) komanso kulimbikitsa ulimi wa mbuzi ndi ng’ombe popeleka kwa ulele kwa anthu mdziko muno.
“Tiyeni loweluka likubwereri tikawalandire Mai Joyce Banda ,mtsogoleri wathu ,yemwe mu nthawi yake yochepa anakwanitsa kusitha miyo ya anthu popeleka zochita monga ulimi wa ziweto ndi kuyambitsa anthu kuchita matola a njinga,tiwavotele kuti adzapitilize izi” anatelo a Mwandira.
Chipani cha PP ndi chimodzi Mwa zipani zomwe ndi zodziwika bwino m’dziko lino ndipo mtsogoleri wake analamulira dziko kwa zaka ziwiri potsatira infa ya mtsogoleri wakale Bingu wa Muntharika yemwe anali wachitatu chiyambireni pomwe dziko lino linachoka mu ulamuliro wa a zungu(atsamunda).
Follow and Subscribe Nyasa TV :