Zoopsa! Azimayi, atsikana akugonana ndi asodzi kuti aziwapatsa milamba, makakana
Atsikana ndi amayi akugonana ndi asodzi pa doko la Bulawayo ku Nsanje n’cholinga choti aziwapatsa milamba ndi makakana.

Mkulu woona za ntchito yolimbana ndi edzi a MacKnowledge Tembo komanso woona za ntchito yogawa makondomu m’bomalo a John Maganizo ndiwo atulutsa nkhaniyi patsiku lokumbukira kufunika kwa makondomu pa msika wa Sorgin m’bomalo.
“Atsikana ndi amayi akapita ku doko la Bulawayo asodzi akumawafunsa: Nsomba mwazipezadi, kodi mupereka ndalama kapena ayi?’
“Akayankha kuti ayi asodzi akumadziwiratu kuti ameneyu akufuna nsomba zosinthana ndi kugonana,” anatero a Tembo.
Mkuluyu wati izi zikuchititsa kuti atsikana ambiri a zaka zapakati pa 15 ndi 24 azipezeka ndi kachilombo ka HIV.
“Kafukufuku yemwe tachita posachedwapa waonetsa kuti kachilombo ka HIV kayambiranso kufala kwambiri pakati pa atsikana a zaka za pakati pa 15 ndi 24,” atero a Tembo.
Ofesi ya zaumoyo yachita kafukufukuyu pa chipatala Sorgin, Kalemba, Mbenje ndi pa chipatala chachikulu cha pa boma la Nsanje.
Bungwe la Aids Healthcare Foundation (AHF) ndilo lidachititsa mwambowo mogwirizana ndi ofesi ya zaumoyo ya m’bomalo.
Mkulu wolimbana ndi kufala kwa kachilombo ka HIV m’chigawo chakummwera m’bungwe la AHF a Jacob Pidini adati mwambowo wachitikira kwa Sorgin chifukwa chakukwera kwa chiwerengero cha anthu atsopano opezeka ndi HIV.
Katswiri wa nkhani zaumoyo pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences a Paul Kingstone Mphepo akuti izi zikuchitika chifukwa mabungwe a zaumoyo anatangwanika ndi matenda a Covid-19 komanso kolera.
“Chofunika apa ndi kupereka mwakathithi mauthenga wothandiza anthu kudziteteza ku HIV,” iwo atero.
Pamwambowo akatswiri azaumoyo anafotokozera anthu kufunika kogwiritsa ntchito makondomu moyenera podziteteza ku HIV ndi mimba zosaziyembekezera.
Nsanje ili ndi anthu 26 000 omwe akulandira mankhwala wotalikitsa moyo a ma ARVs.
Tsiku lokumbukira kufunika kwa makondomu pa dziko lonse limakhala pa February 13 chaka chilichonse koma bungwe la AHF lidakonza mwambowu pa February 19.
Follow and Subscribe Nyasa TV :