A Trapence a HRDC akuti kusowa kwa kwa mafuta nchizindikiro kuti boma lalephera

Bungwe la HRDC lati vuto la kusowa kwa mafuta lomwe dziko lino likukumana nalo, ndi chizindikiro kuti boma lalephera.

Trapence

Mu chikalata chomwe chasainidwa ndi wapampando wa bungweli a Gift Trapence, vuto la mafutali silinakhudze Amalawi okha koma lakhudzanso chuma cha dziko lino chomwe chili kalenso pa mavuto a dzaoneni.

HRDC yati kulephera kwa boma kukonza vutoli ndi chizindikiro choti boma lawalephera Amalawi komanso kuti likusowekera ukadaulo oyendetsa ntchito za boma.

Vuto la kusowa kwa mafuta malinga ndi HRDC, ladzanso pomwe Amalawi akudutsa kale mu zokhoma monga kukwera kwa mitengo ya zinthu, kusowa kwa ntchito komanso njala.

HRDC yati zomwe zikuchitikazi zidzetse manyazi kuboma chifukwa nzochititsa manyazi. “Amalawi akufunika boma lomwe lingawatsogolere osati boma lomwe silidziwa kanthu,” atero a Trapence.

Chikalatachi, chauza nduna yoona za mphamvu ya magetsi a Ibrahim Matola kuti angotula pansi udindo ngati sakwanitsa kukonza vuto la magetsi komanso mafuta.

Auzanso boma la a Lazarus Chakwera kuti lipeze mayankho a Amalawi, chifukwa HRDC siyilora Boma lomwe silikudziwa zochita.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
DoDMA prepositions search and rescue equipment in all flood-prone districts

In a significant move to bolster disaster preparedness, the Department of Disaster Management Affairs (DoDMA) has prepositioned essential search and...

Close