Achinyamata sakuonetsa chidwi chopeza nawo ngongole ya NEEF–Watero mkulu wa NEEF a Mdyetseni
Bungwe lopeleka ngongole la NEEF lati ndilokhudzika ndi kuchepa kwa chiwelengero cha achinyamata omwe akuonetsa chidwi chotenga nawo ngongole zake m’dziko muno.

Mkulu wa bungwe a Humphrey Mdyetseni anena izi pa mkumano wolimbikitsa ndi kudziwitsa achinyamata za ubwino wotenga ngongole ya NEEF la Chiwiri mu mzinda wa Blantyre.
Amdyetse ati mwa ngongole za ndalama zokwana K244 Billion m’mdziko muno zomwe zagawidwa mzinda wa Blantyre watengapo K12 Billion momwe amayi oposa 80 pa 100 aliwonse komanso abambo oposa 70 pa 100 aliwonse aonetsa chidwi potenga nawo ngongolizi pomwe anyamata 67 okha pa 100 ndiwo atenga nawo.
“Mzodandaulitsa kuti muzolinga zanthu popeleka ngongole ya NEEF ndi kutukula achinyamata ,koma achinyamatawo sakuonetsa chidwi,chiwelengero chawo mchochepa zedi poyerekeza ndi abambo ndi amayi Maka mu mzinda uno wa Blantyre” anatero a Mdyetseni.
Iwo atinso kwa achinyamata omwe atenga ngongolezi ambiri ayiwo ngakhale kabwezedwe kakukhala kuvuta zomwe ati zikufunikira kuti achinyamatawa aphunzitsidwe bwino za kufunika komanso kuunikilidwa za kabwezedwe Ka ngongolezi akatenga.
“tiyamikireko achinyamata a madera monga Limbe pomwe akukwanitsa kubweza moyenerera ngongole akatenga ,komabe takonzeka kulimbikitsa, kuphunzitsa achinyamata ena pomwe zikuvutavutabe kuti nawo atengelepo chitsanzo cha anzawo enawa” anatsindika motero a Mdyetseni.
Apa mkulu wa bungweyu watinso alimbikitsa za ulimi pomwe achinyamata azipatsidwa ngongole komanso zipangizo zosiyanasiyana ngati mbali imodzi yakonzera vutoli pakati pa achinyamatawa.
Iwo atinso pofika lero alimi pomwe ambiri ndi abambo ndi amayi oposa 26,000 afikilidwa kale ndi thandizili ndipo bungweli layerekeza kufikira alimi 100,000 pofika mwezi wa September m’chakachi.
Iwo ati iyi ndi mbali inà yothandiza boma pa ntchito yowonetsetsa kuti chakudya Chikupezeka chokwanira mdziko muno.
M’mawu ake mlembi wa gulu la a achinyamata a mu mzinda wa Blantyre,Alinafe Nkhata anayamikira NEEF kamba kokonza mkumano wa maphuziro alimbikitsa achinyamata mu mzindawu komanso kamba kowanganizira kuti nawo apeza ngongozerezi komanso zipangizo za ulimi ponena kuti izi zasitha miyoyo yawo mu zambiri.
“Tiyamikire bungwe la NEEF potipatsa mwayi oti Nafe tapeza ngongole komanso kuti izi zipitiliranso kwa ena pomwe sanathe kupeza nawo mwayiwu ,koposaposa potipatsanso upangili wa tsopano pa nkhani za ngongolezi ndi Katundu yemwe tidzigwiritsa mu ulimi ” anatero a Nkhata.
NEEF ndi bungwe lomwe kale linkadziwika ndi dzina loti Malawi Enterprise Development Fund yomwe linakhazikitsidwe pansi pa malamulo oyendtsera makampani omwe anakhazikitsidwa m’chaka cha 2013(Companies Act of 2013).
Follow and Subscribe Nyasa TV :