Chakwera athandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi yodza kamba kosefukira kwa madzi

Tate wa pfuko la Malawi , Dr Lazarus McCarthy Chakwera lero wapereka katundu osiyana siyana kwa anthu omwe akubvutika ndi madzi osefuka mboma la Karonga.

Chakwera wapereka ufa , ziwiya zophikira , ndiwo ndi katundu winanso kwa ndi cholunga choti anthu kumeneko athandizike mdelaro.

Poyankhula atayendera misasa ya Kambwe ku Karonga, komweko , mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera adatsimikizira anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi m’derali kuti akambirana ndi gulu lankhondo la Malawi Defence Force (MDF) ndi maunduna omwe ali ndi udindo kuti amange khwawa   kuti athane ndi vuto lakusefukira kwa madzi omwe amabwela mwa  mphamvu kuchokera ku  mtsinje wa Rukuru.

Iye adati iyi ndi njira yokhayo yoteteza derali kuti madzi asamasefukire, .

Mtsogoleri wa dziko lino yemwe ali ndi wachiwiri wake Dr Saulos  Chilima wawuza athu omwe ali pa msasawo  kuti akanene ku akuluakulu aboma ngati papezeke wina  akugwiritsa ntchito nthandizo molalikwika kuti apindure.

Dr Chakwera adapitiliza kuthokoza mabungwe ndi anthu omwe akugwira ntchito usana ndi usiku pofuna kuonetsetsa kuti anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi akupeza zinthu zofunikira.

Mtsogoleri wa dziko lino wapereka ziwiya zakukhitchini, chimanga ndi ufa wa chimanga mwa zina kwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

Mvula yamphamvu yomwe idagwa mowirikiza idaononga katundu wambiri ku Karonga ndi ku Nkhotakota.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Mwanamveka tears budget apart, says economy can’t grow but 4.8% in 2025

DPP spokesperson on Finance Joseph Mwanamvekha says the assumption that the local economy will grow by 3.6 percent in 2024 ...

Close