Chakwera atsekulira misika ya fodya ku Kasungu lero

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera agwira ntchito zosiyana siyana m’boma la Kasungu lero kuwonjezerapo kutsegulira m’sika wa fodya, malingana ndi chikalata watulutsa mlembi wamkulu wa boma mayi Colleen Zamba.

Chakwera

A Chakwera akuyembekezeka kuyendera nyumba za asirikali a nkhondo zomwe boma la Malawi Congress (MCP) lamanga ku Engineering Battalion.

Malingana ndi chikalatachi, mtsogoleri wa dziko lino akatseguliranso ofesi ya bungwe La Tobacco Commission lomwe lamangidwa m’boma la Kasungu.

Akakachoka ku ku ofesi ya TC , m’boma La kasungu mtsogoleri wa dziko lino akayendera fodya ku msika wa fodya wa Chinkhoma.

Pomaliza pa zonse mtsogoleri wa dziko lino akatsegulira msika wa fodya pa sukulu ya vivya mdela la mfumu yayikulu Njombwa pomwe akulu aboma ndi abungwe la TC akuyembekeza kukayankhula.

Kasungu ndi boma limodzi lomwe limatchuka kwambiri pankhani za ulimi wafodya kuyambira nthawi yomwe mtsogoleri wa kale wa Dr Hastings Kamuzu Banda adali moyo.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Police arrest Nun attacker, says he is a mentally ill person

Police say they have arrested a 38-year-old man for allegedly attacking a Catholic nun in Zomba on Thursday. National police...

Close