Chipani cha UTM chatsimikiza kuti chikukapanga mwambo woyatsa makandulo pamalo pomwe ndege inagwera
Chipani cha UTM chati chakonza mwambo oyatsa kandulo kufupi ndi malo amene ndege imene anakwera Saulosi Chilima inagwera ku Mzimba mmawa lino.

Mlembi wamkulu wachipinichi, Patricia Kaliyati wauza Nyasatimes kuti mwambowu ndi mbali imodzi ya zochitika zimene chipani chawo chakonza pofuna kukumbukira mtsogoleri wawo.
Chihaula Shaba, m’modzi mwa akuluakulu a chipani cha UTM mchigawo chakumpoto wauza Nyasatimes kuti mwambowu udzachitikira pa sukulu ya Primary ya Nthungwa imene ili m’mudzi oyandikana ndi malo amene ndege imene anakwera Chilima komanso anthu ena asanu ndi atatu inagwera mu nkhalango ya Chikangawa.
Shaba wati mwambowo udzayamba chakum’mawa ndi mapemphero, kenaka padzakhala zoyankhulayankhula.
Chihaula watinso malingana ndikuti ku Chikangawa ndi kutali, anthu onse amene adzakhale nawo pa mwambu adzalandira chakudya