Clement Nyondo wafika ku Wanderers, wasayina mgwirizano wa zaka zitatu
Katswiri osewera ku tsogolo, Clement Nyondo, wasintha thabwa tsopano pamene walowa timu ya Mighty Wanderers potsatira kuchoka ku timu ya Dedza Dynamos.

Nyondo, amene ali ndi zaka 23 ndipo anatenga mphoto ya katakwe omwetsa zigoli zambiri ( Golden Boot Award) mu TNM Super League ndi zigoli 16 chaka chatha, wasayina mgwirizano wa zaka zitatu ku Lali Lubani kufikira chaka cha 2027.
Nkhani ya msamuko wa osewerayu inavuta masiku apitawa pamene bungwe la FAM linanena kuti ali ndi mgwirizano odzatha chaka cha 2025 ku timu ya Dedza Dynamos, koma mwini wake amati mgwirizano wake ukutha pa 05 February chaka chino.
Akuluakulu a mbali zonse ziwiri akana kuwulura ndalama zimene asinthana pa malonda a mnyamatayu, koma timu ya Dedza Dynamos inakhazikitsa mtengo wa 15 million Kwacha.
Zinamvekanso kuti Nyondo, amene anadziwika kwambiri ali ku timu ya Karonga United, amafunidwanso ndi ma timu a Singida ya ku Tanzania komanso Kabwe Warriors ya ku Zambia ndinso Silver Strikers.
Follow and Subscribe Nyasa TV :