Kukweza maphunziro: Boma lakweza malipiro aphunzitsi othandizira ndi theka, nkulembanso ntchito ena 4 200

Mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera waonetsa chidwi chake pankhani ya maphunziro.

Ichi nchifukwa chake Boma kudzera ku Unduna wa Zamaphunziro lakweza malipiro apamwezi a aphunzitsi othandizira (Auxiliary Teachers) ndi theka la ndalama zomwe amalandira m’mbuyomu kuchoka pa K80, 000 kufika pa K120,000, komanso alemba ntchito ena okwana 4, 200.

Kalata yomwe wasayinira ndi Mlembi Wamkulu mu undunawu, Dr Mangani Chilala Katundu, yati aphunzitsi othandizirawa, alembedwa ntchito pa mgwirizano wa chaka chimodzi pansi pa ndondomeko yotukulira maphunziro a kupulayimale ya Malawi Education Reform Programme (MERP).

Iwo ati aphunzitsiwa achokera kumagulu a Initial Primary Teacher Education (IPTE) a 14, 15 ndi 16 ndipo omwe akonzeka kukagwira ntchitoyi m’malo osiyanasiyana kuyambira mwezi wa Sepitembala chaka chino.

Potsimikiza za kalatayi Mneneri mu undunawu a Mphatso Nkuonera, ati mndandanda wa sukulu zokaphunzitsa aphunzitsiwa ukupezeka m’boma lirilonse kumaofesi oyendetsa zamaphunziro.

Mneneriyu anati iyi ndi imodzi mwa njira zomwe boma latsata pofuna kuonjezera chiwerengero cha aphunzitsi oyenerera msukulu za pulayimale za m’dziko muno.

“Kutenga nawo mbali kwa aphunzitsi othandizira ndi kwa chaka chimodzi basi ndipo sizikutanthauza kuti adzalembedwa ntchito yokhazikika ikatha nthawi yawo,” atsindika a Nkuonera.

Kulemba ntchito aphunzitsi othandizira ndi gawo limodzi la pologalamu ya MERP yomwe ikumanganso zipinda zophunzilira zokwana 10,900, zipinda zaukhondo 1000 dziko lonse, kuphunzitsa atsogoleri a m’sukulu kuti aziyendetsa bwino sukuluzo, komanso kupereka ndalama zoyendetsera ntchito zina za pasukulu.

Ndondomeko ya MERP imalandira thandizo lake kuchokera ku Boma la Malawi, Banki Yaikulu pa Dziko lonse komanso ku Mgwirizano wa Mabungwe azamaphunziro (Global Partnership for Education)

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Prophets accuses PAC of attempting to policies prophecies

The Prophetic Ministries Association of Malawi (PROMAN) has hit back at the Public Affairs Committee (PAC) for attempting to regulate...

Close