Kwa Nkope ku Mangochi kuli chiopsezo cha matenda otsegula mimba

Anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukila kwa madzi ku Nkope m’boma la Mangochi ati miyoyo yawo ili pa chiopsezo chodwala matenda otsekula mmimba ngakhale kufa ndi njala kumene.
Anthu-wa omwe akukhala ku misasa ati nyumba zawo, zimbuzi, chakudya mwa zina zinaonongeka ndipo akusowekera thandizo la msangasanga.
Iwo ati akumwa madzi osatetezeka komanso anthu akumangozithandiza paliponse kaamba koti zombuzi zawo zidakokolola ndi madzi.
Mayi Jamira Alafati ati adandaula kuti pambali pa kusowa kwa madzi aukhondo ndi zimbuzi akusowa chakudya, zomwe ati zichititsa kuti ana ambiri adwale matenda osowa chakudya mthupi.
” Ngati sipapezeka thandizo la msangamsanga la chakudya, matenti, mankhwala ophera tizilombo mmadzi akumwa kuno kubuka matenda ndipo anthu amwalira” watero khansala wa delari Ali Mohamed.
Apa Khansala-yu wapempha nthambi yoona ngozi zogwa mwazizizi ya Dodma kuti igwepo mwamsanga kuti kupulumutsa miyoyo.
Mbuyomu ofesi ya bwanamkubwa m’boma la Mangochi inalengeza kuti motsogozedwa ndi Dodma yayambapo kufikila ndi thandizo losiyanasiyana kwa anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukila kwa madzi.
Maanja ochuluka ku Mangochi akusowa pokhala kaamba ka kusefukila kwa madzi komwe kwadza chifukwa cha kukwera kwa madzi myanja ya Malawi komanso nsinje wa Shire.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Report exposes that very little of approved funds in the education sector is being disbursed

Disbursement and utilisation of funds in the country’s education sector is fraught with significant discrepancies with little of the approved...

Close