Mafumu apereka Ndodo ya ulemu ya Umbuya kwa a Illias Karim

Mafumu a ndodo a boma la Chikwawa komso Nsanje ati tsopano ndiwokhutira ndi ntchito za phungu wa kunyumba ya malamuro wa mdera la kumwera kwa boma la Chikwawa a Illias Karim.

Polankhula ndi ena mwa mafumu a ndodo a maboma a Chikwawa ndi Nsanje, Mfumu yaimkulu Ngowe anati a Karim ndi phungu yekhayo amene amakonda anthu ake mderalo komaso kukhala nawo limodzi pa nthawi yonse iwo akamatumikira mderalo.

Malingana ndi Mfumu yaimkulu Ngowe, phunguyu pambali pa izi ndi wa chitukuko kwambiri zomwe zapangitsa mdera lake kukhala ndi ntchito za chitukuko zochuluka kuyambira zitukuko za umoyo, maphunziro, madzi abwino, magetsi mwa zina.

Boma lathu la Chikwawa muli madera asanu ndi awiri (7) a phungu akunyumba ya malamuro koma mwa aphungu amenewa, a Karim ndi yemwe waonetsa kukhala wa chitukuko kuposera amzawo onse komaso wa chikhalidwe chabwino moti ifeyo ngati mafumu timakondwera nawo.

Pena ndi bwino kumuyamikira mwana wa mzako akapanga zinthu zabwino. Ife ngati mafumu a boma la Chikwawa tikupereka ndondo ya ulemu ya umbuya kwa a Karim zomwe zitanthauze kuti ndi munthu yemwe angayang’anire anthu a bomali mosatengera chipani, chipembedzo kapena mtundu, ‘’anatero Mfumu yaimkulu Ngowe.

Kumbali yawo, Senior Chief Chimombo ya boma la Nsanje anati iwo alibe mvuto ndi kuperekedwa kwa ndodo ya ulemu ya umbuya kwa a Karim.

Iwo anati a Karim ndi wa ndale yekhayo ochokera maboma akuchigwa kwa mtsinje wa Shire yemwe waonetsa ntchito zake za bwino potumikira anthu komaso kukhala bwino ndi anthu onse a maboma awiriwa kotero akuyenera kukhaladi mbuya wathu pa ndale.

Senior Chief Chimombo anapitiriza kunena kuti posachedwapa akamaliza zokambirana ndi mafumu amzawo a maboma awiriwa akoza mwambo wa padera okapereka ndodoyo kwa a Karim yomwe idzatsikimizire ulemu wa umbuya wa maboma wa.

Ndikufuna ndilankhule mopanda nkhwidzi kuti a Karim tsopano alowa malo mwa malemu Sidik Mia yemwe anali mbuya wathu kutsatira imfa ya mbuya Gwanda Chakuwamba ndipo lero a illias Karim nawoso akulowa malo mwa a Sidik Mia kutsatira imfa yawo,’’anatero Senior Chief Chimombo.

Malingana ndi Senior Chief Chimombo, ulemu wa umbuya sumatengera kukhala ndi mzaka zochuluka zobadwa popereka zitsanzo za a Gwanda Chakuwamba komaso a Sidik Mia kuti anapatsidwa umbuya koma analipo ena a mzaka zochulukirapo kuposera iwowa koma ntchito zawo ndi zomwe zidapangitsa mafumu a maboma wa kupereka ndodo ya ulemu ya umbuya kwa iwowa.

Poyankhapo pa nkhaniyi, a Illias Karim anathokoza mafumu kamba ka mtima wawo wa chikondi poyamikira ntchito zawo.

Iwo anati palibe tsiku lomwe anaganizapo kuti mafumu amaboma awiriwa amawaonera munjira ina yabwino ngati apangiramu ndipo alonjeza kugwirira ntchito limodzi ndi mafumu komaso anthu onse pofuna kuonetsetsa kuti maboma awiriwa akupita pamtsogolo pa ntchito za chitukuko.

Kumbali ya ulemu ya ndodo ya umbuya yomwe mafumu amaboma awiriwa agwirizana kuti awapatse ngati ulemu wawo, iwo anati kwawo ndi kuyamikira ngati mene alankhulira kale kuti sanayembekezere kumva zomwe mafumu wa alankhula pa ntchito zawo.

Ndodo ya ulemu ya umbuya kuchokera kwa mafumu a ndodo a maboma a Chikwawa ndi Nsanje kuperekedwa kwa munthu opanga ndale limatanthauza kukhwima mzeru pa ndale kwa munthuyo popanga zinthu komaso kuthandiza anthu moyenerera a maboma wa.

A Illias Karim anayamba ndale ali ndi mzaka 23 zakubadwa poyimirira pa chisankho chawo choyamba cha uphungu cha mdera la kumwera kwa boma la Chikwawa cha mchaka cha 2014 ndipo adapambana ndi mavoti 9,811.

Pa chisankho chawo cha chiwiri cha mchaka cha 2019 iwowa adapambanaso ndi mavoti okwana 15,927 ndipo pa chisankho cha chitatu cha mchaka chino cha 2025 chomwe zotsatira zake zosatsikimizika sizinalengezedwe koma zikuonetsaso kupambana kwawo ndi mavoti okwana 24,833.

 

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter

Leave a comment

Your email address will not be published. Required fields are marked *