Mfumu Piyasani 2 yabela ndalama anthu olandila mtukula pakhomo kwa Mtsiliza ku Lilongwe

Anthu ochuluka kwa Mtsiliza mu mzinda wa Lilongwe, makakaka mmudzi wa a Senior Group Piyasani 2, akulira ndipo ndi odandaula kaamba koti mfumuyi inatenga ndalama kwa anthuwa kuti akhale nawo mkawundula wolandila ndalama za mtukula pakhomo.

Omwe akuyimilila anthu okhuzidwawa, Moses Kalipinde ndi Josen Kamwera, ati mfumuyi yinalandila ma MK5,000 ndi ma MK10,000 kwa anthuwa.

Izizi akuti zinachitika masabata pafupifupi awiri apitawo.

Awiriwa ati anthu obeledwa ndi mfumuyo alipo ambiri koma khumi ndi atatu okha ndi omwe pakali pano alimba mtima nkubwera poyela kufotokoza za umbavawu

“Mmodzi mwa anthu obeledwawa, amene ali ndi mwana wa ulumali ndipo ndi ovutika zedi, ndiamene anatisina khutu. Choncho ife zinatikhuza kwambiri mpomwe tinaganiza zoyitengala nkhaniyi patali”.

A Kalipinde ndi a Kamwera afotokozanso kuti anakaneneza mfumuyo ku Lingadzi Police Station, komwe kufikila lero sanawathandize pa nkhaniyi.

“Mfumuyi sikutengedwa ndi a polisi,” atero awiriwa ndipo awonjezara kuti nkhaniyo anakayitulanso ku Lilongwe City Council, ku bungwe la Anti Corruption Bureau, ku DoDMA, NICE Trust ndi ku office ya bwana nkubwa wa Lilongwe, komwe sakuwathandizanso.

“Palibe chomwe chikuchitikapo. Mfumu yokubayo ndi mfulu mpakana pano, palibe aluchitapo ma office onsewo ndipo zonsezi zikulimbikitsa mchitidwe woyipa wa mfumuyi.

“Choncho tikupempha mabungwe ndi anthu akufuna kwabwino kuti atithandize kuti chilungamo chioneke, anthu awabwezele ndalama zawo”.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Mounting pressure on Chakwera to institute inquiry into plane crash: MHRC joins the fray

As calls for accountability intensify, President Lazarus Chakwera faces growing pressure to establish a commission of inquiry into the plane...

Close