Tiyambaso kunyanyala ntchito, ogwira ntchito za umoyo muzipatala za boma awopseza mabwana awo

Ogwira ntchito za umoyo mdziko muno achenjeza kuti ayamba kachikena kunyanyala ntchito mu zipatala zonse za boma mdziko muno.

Minister of Health Khumbize Kandodo Chiponda and health workers

Izi zikudza pomwe bungwe la oimila ogwira ntchito za umoyo-wa la Physician Assistant Union Of Malawi linati silokhutila kuti boma likulephera kukweza ndalama za alawansi mofanana ndi momwe anagwirizana ndi akuluakulu aku unduna wa za umoyo.

 

Poyankhula, Solomon David Chomba wati, m’buyomu ogwira ntchito atangoyamba kunyanyala ntchito posakondwa ndi kuchedwa kwa boma kukweza ma alawansi-wa, boma linapita kubwalo la milandu kukatenga chilolezo choimitsa kunyanyala ntchito-ku.

 

Chomba wati owaimila awo pa milandu ali mkati mochotsa chiletsochi ku bwalo la milandu, ndipo ati chikachitsedwa ayambilanso kunyanyala ntchito mu zipatala zonse.

 

“Funa ndiuze a Malawi onse komanso Boma kuti ayembezekere kuti awona kunyanyala ntchito kwa aza umoyo mu zipatala zonse za mdziko muno komwe sanakuonepo chiyambileni chifukwa takwiya,” watero Chomba”.

 

Iwo ati pa nthawi-yi sipadzapezeka wa za umoyo yemwe adzagwile ntchito, ndipo mmalo mwake akuti adzidzauza odwala onse kuti adzidzapita Ku ma ofesi akuluakulu awo omwe akulandira ma alawansi ochuluka kuti akawathandize.

 

Tinayesetsa kuti tiyankhulane ndi akuluakulu aza umoyo koma sizingatheke

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Vice president Usi demonstrates his respect for Chilima: Retains the staff that worked for Chilima

In a rare gesture of political maturity, recently appointed Vice President Michael Usi has retained all staff members who worked...

Close