Usi ayankhulapo pa imfa ya Lucius Banda: “Ntchito za Lucius zinali zozama kotero kuti zipitilira kutumikira’
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Michael Usi wati ndiwokhudzidwa ndi imfa ya mkhalakale mu maimbidwe Soldier Lucius Banda.

Mukalata yomwe alemba, a Usi ati akulira limodzi ndi mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera komanso Amalawi onse.
Iwo atinso banja la chipani cha UTM lataya munthu yemwe amatsogolera ntchito zokopa anthu mu chipanichi komanso membala wamkulu.
A Usi ati dziko la Malawi likudutsa mu nyengo yosautsa ndipo akupempha Mulungu kuti atipatse mphamvu komanso nzeru.
“Lucius anali mkhalakale mu maimbidwe komanso amazipereka pa ntchito ya chipani.
“Ntchito za Lucius zinali zozama kotero kuti zipitilira kutumikira,” atero a Usi.
Follow and Subscribe Nyasa TV :