A polisi amanga anthu awiri pokuva ndalama pafupifupi K111 million kwa munthu yemwe anawapasa lift
Anthu awiri ali mchitokosi cha polisi ku Lilongwe powaganizira kuti anali nawo m’gulu la anthu anayi omwe adabera munthu yemwe anakwera galimoto yawo ndalama yokwana 64 000 dollars (pafupifupi K111 million).
Apolisi apezaponso K5 million pa ndalama yobedwayo komanso galimoto la mtundu wa Honda Fit ya ndalama pafupifupi K10 million, yomwe akuganizira kuti idagulidwa ndi ndalama zakubazo.
Oganiziridwa omwe agwidwawa ndi a Joseph Kamanga a zaka 32, omwe ati amatchuka ndi dzina loti Ntonga kuchokera m’mudzi wa Kabunduli ku Nkhata Bay, wina ndi Symon Botoman wa zaka 31 wochokera m’mudzi wa Sinde ku Kasungu.
Mneneri wa polisi ya Lilongwe Hastings Chigalu wati pa 25 April cha m’ma 9 koloko m’mawa, bambo wina wochita malonda anaima pa malo wokwelera galimoto pafupi ndi ma ofesi a MRA omwe ali m’mbali mwa nsewu opita ku Mchinji, ndicholinga choti akwere galimoto kukasiya ndalamayo kwa mzake ku Mchinji.
Posakhalitsa anayiwo anafika pa galimoto yawo nkuuza mkuluyo kuti akwere ati ponama kuti galimoto yawo inali taxi yomwe imanyamula anthu kupita ku Mchinji boma.
Koma atayenda pang’ono kufika pa stage ya Mango, anaima n’kuuza mwini ndalamayo kuti atsike popeza sapitilira, koma akulimbama ndi chitseko kuti atsike, anthuwo akuganiziridwa kuti anatsegula chikwama ndi kutengamo ndalamazo.
Woberedwayo anadziwa pambuyo pake atatsika kale galimotoyo kuti waberedwa ndalama.
Atakadandaula ku polisi, apolisi ya Lilongwe mu ukadaulo wawo anafufuza ndi kukamanga oganiziridwawa ali mu mzinda wa Mzuzu ndi kupeza galimotoyo. Apolisi akusakabe anthu ena awiri omwe akuganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyi.