Achinyama enanso 140 wapsa wa ku Israel: Katswiri akhuzidwa akuti boma likuchulusa chinsinsi

Achinyamata okwana 140 akuyembekezeka kunyamuka mdziko muno lachitatu kupita ku Israel komwe azikagwira ntchito ku minda.

  • Yatera kale ndege ija

Koma olankhulapo pa nkhani za ufulu,  a Michael Kayiyatsa ati pomwe ndondomekoyi ndi yabwino, boma likuyenera kumachita machawi kufotokozera anthu momwe ntchito yotumiza achinyamata ku Israel ikuyendera kuopa manong’onong’o.

Ngakhale zili choncho, aJustice Kangulu omwe ndi mkulu wa kampani yopezera anthu ntchitto ya Arama yomwe ikuyendetsa ntchitoyi, atsimikiza kuti achinyamatawa akuyembekezeka kunyamuka pa bwalo la Kamuzu kupita ku Israel m’bandakucha wa lachitatu.

Iwo ati pomwe amasayina mgwirizano wa ntchito,  achinyamatawo awalongosolera mwa mvemvemve, zomwe akuyenera kuyembekezera komanso zomwe mabwana awo akuyembekezera akapita ku Israel.

Malinga ndi nduna yofalitsa nkhani mdziko muno a Moses Kunkuyu,  achinyamata oposa 700 ochokera mdziko muno ali ku Israel komwe akugwira ntchito mu ndondomeko yotumiza ogwira ntchito mmaiko ena.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
CFTC says some distributors hoarding sugar, warns of action

The Competition and Fair Trading Commission (CFTC) has said some distributors are hoarding sugar, a conduct which the consumer protection...

Close