Amangidwa pobera mkazi mafoni atamunamiza kuti amukwatira, komanso alemera ndichizimba

Apolisi ku Lilongwe amanga a Thokozani Charles, powaganizira kuti adaba mafoni awiri a mayi wina atamunamiza kuti amukwatira komanso kuti alemera akachita zizimba.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu wati mkuluyu, yemwe amachita malonda ogulitsa zovala, adakumana ndi mayiyo pa tsamba la mchezo la Facebook sabata ziwiri zapitazo.

Kenaka akuti adakakumana ku malo ogona alendo ku Area 50, komwe adakasangalatsa matupi awo. Madzulo ake adauza mayiyo kuti apite malo ena akapange matsenga woti apeze chuma monga banja.

Malinga ndi lipoti la polisi, atafika pa malo oyandikana ndi bwalo la za masewero la Bingu National Stadium, woganiziridwayu adauza mayiyo kuti akachite zizimba pa mphambano.

Apa ndipomwe woganiziridwayo adathawa ndi ma foni awiri a ndalama pafupifupi K300 000 omwe apolisi awapeza kale.

Mayi woberedwayo, yemwe amakhala ku Area 23, adakamang’ala kwa apolisi omwe adamanga a Charles atawapeza akupha tulo ku nyumba kwawo ku Mtandire.

A Charles ndiochokera m’mudzi wa Chitenje ku Zomba.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Subscribe
Notify of
guest

0 Comments
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
0
Would love your thoughts, please comment.x
()
x
Read previous post:
MCP condemns DPP Parliamentarian Daud Chikwanje over the careless statement of “Otchani a MCP”

Malawi Congress Party (MCP) Secretary General Richard Chimwendo Banda has condemned Democratic Progressive Party (DPP) law maker , Daud Chikwanje...

Close