Amangidwa popotokola khosi la mwana wawo pofuna kukhwima kuti alemere
Apolisi ku Nathenje, Lilongwe amanga mayi wa zaka 25 a Ivy Elinati komanso mamuna wake wa zakanso 25, a Mphatso Nalinde, powaganizira kuti adapotokola khosi nkupheratu, mwana wawo wa zaka ziwiri pofuna kukhwima kuti alemere.
Mneneri wa polisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu ati a Elinati ndi mayi wa mwanayo ndipo a Nalinde anali bambo ake ompeza.
A Chigalu ati awiriwa amafunitsitsa kulemera ndipo adakambirana ndi sing’anga wina wa ku Mozambique yemwe adawauza kuti aphe mwana wawoyo kuti apangire mankhwara.
“Banjalo lidatsanzika anthu mmudzi kuti akupita kukayendera achibale ku Mozambique ndipo atafika panjira, adapotokola khosi nkupheratu mwanayo. Koma ataimbira foni sing’angayo kumuuza kuti apha mwanayo ndipo akupititsa thupi lake, sing’angayo adakana kuti asapitenso ndi thupilo ponena kuti asemphanitsa chizimba,” atero a Chigalu.
Iwo ati banjalo lidabwelera ndi thupi la mwanayo kumudzi komwe atauza mafumu kuti mwanayo adawafera panjira, mafumu sadavomele ndipo adakanena ku polisi.
“Achipatala atayeza thupi la mwanayo apeza kuti adafa kutsatira kubanika komwe kudachitika chifukwa chopotokoledwa khosi. Sing’angayo pakadali pano sadadziwike,” atero a Chigalu.
Follow and Subscribe Nyasa TV :