‘Andale, atolankhani, a mpingo tiyeni tisafune kutchukirapo pankhani ya kusowa kwa ndege’

Mneneri wa boma a Moses Kunkuyu apempha andale, atolankhani, anthu apa social media, komanso amipingo kuti asafune kutchuka pa nkhaniyi pokhala patsogolo kumafalitsa nkhani zobweresa kusiyana mdziko pamene ntchito yosanga ndege ili mkati.

A Kunkuyu anena izi pomwe amachitisa msonkhano wa atolankhani mamawa uno pamodzi ndi mkulu wa asilikali a Valentino Phiri ku Lilongwe pa nkhani yakusowa kwa ndege.

A Kunkuyu ati mafoni a anthu omwe adali mu ndegeyi akuonetsa kuti amachita ‘register’ pa tower ya mu Chikangawa ndipo nchifukwa chake akulimbikira kusaka malowa. Ndipo anawonjexerapo kuti a Macra adasakasaka mafoniwo ndipo Macra yapemphanso ukadaulo wa maiko ena monga Angola kuti athandize kusaka ndegeyi.

Polankhulapo, a Phiri ati uthenga omwe ali nawo ndiwoti ndegeyi yagwera mu Chikangawa ndipo iwo chidwi chawo chili posaka mnkhalangoyi.

Apolisi, a za nkhalango ndi civil aviation (a za ndege) akuthandiza pa ntchitoyi, atero a Phiri. Iwo ati kuchoka dzulo, sanapeze chilichonse mpaka pano. A Phiri ati komwe kukuganizilidwa kuti kwagwera ndegeyi, sikukhala anthu ndipo ndi nkhalango yowilira kwambiri zomwe zikuchititsa kuti kusakaku kukhale kovuta.

Iwo atinso malowo kuli chifunga kwambiri chifukwa cha nyengo yovuta yomwe yakuta malowo. Mkulu wa asilikali watinso okwana 200 akugwira ntchitoyi koma akukumana ndi mavuto a nyengo ku malowo.

Iwo ati anthu enanso omwe sakudziwa kanthu pa zomwe zikuchitika akusokoneza ntchitoyi polankhura zopanda umboni. A Phiri ati nkhani yabwino ndi yoti mayiko otizungulira akubweletsa thandizo kuti kusaka ndegeyi kukhale kosavuta.

First Capital Bank ati yathandiza ndi ndege yake komanso sukulu yaukachenjede ya MUST nayo ikuthandiza. A Phiri ati MDF ndiyomwe ikugwira ntchitoyi ndipo anthu adzidikira kumva kuchoka ku MDF

 

 

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
UTM pushes Govt for more effort in tracking the plane: Wonders why transponder not working

Visibly sad and distressed, UTM Secretary General Patricia Kaliati wants government to exert more effort in tracking, wondering why the...

Close