Anthu 6 amwalira Kamba kamadzi osefukira ku Nkhota Kota, mabanja 17 176 akhuzidwa

Chiwerengero cha anthu omwalira ndi ngozi ya madzi osefukira m’boma la Nkhotakota chakwera kufika pa 6 komanso ena anayi avulala.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe nthambi ya boma yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA yatulutsa pa ngozi yomwe inachitika sabata latha.

Anthu okwana 14,176 anakhudzidwa ndi ngoziyi pamene ena 9,378 akusungidwa pamene nyumba zawo zinaonongeka ndi madzi osefukira.

Mwa anthu omwe akusungidwa mmisakasa 1,638 ndi ana omwe sanakwanitse zaka zisanu, amayi poyembekezera 287, amayi oyamwitsa oposa 305 aulumali komanso 82 okalamba.

Mneneri wa nthambi ya DoDMA Chipiliro Khamula watinso mwa anthu okhudzidwawa, 7,189 ndi abambo pamene 6,987 ndi amayi.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Mzuzu youth postpones its passport demonstrations: Says Chakwera’s presence raises security concerns

The Mzuzu Youth Caucus has postponed its demonstrations that were planned for Thursday, March 7th, 2024 due to security concerns....

Close