Anyamata ofuna kupita ku Israel akwiyira boma Kamba kowachedwesa kupita

Achinyamata okwiya asonkhana pa manda a Kamuzu ku Lilongwe pomwe akufuna kuyamba ulendo wawo opita ku nyumba ya chifumu {Kamuzu Palace} kuti akatule madandaulo awo pa nkhani ya ulendo wawo waku Israel.

Iwo akuti adapanga zonse zoyenera monga kupangitsa ma passport kuti akagwire ntchito ku minda yaku Israel koma ndondomekoyi ikuchedwa ndipo akuona kuti zalowa ndale.

M’modzi mwa achinyamata omwe akutsogolera gululi, a Thomson Msosa wati analembetsa zokagwira ntchito ku Israel mwezi wa November chaka chatha koma mpakana pano sadanyamukebe.

“Tinatenga ngongole pomwe timakonzekera ulendowu ndipo eni ake ndalamazo akuvutitsa. Ife angotilora tidzipita, adzipanga zokambirana zawozo ife titapita,” watero Msosa.

Padakalipano, galimoto ya polisi yatenga ena mwa atsogoleri awo kupita nawo ku ofesi ya DC wa munzinda wa Lilongwe.

Izi zikudza patatha sabata ziwiri boma litalengeza kuti likuchita zokambirana ndi dziko la Israel kuti asainirane mgwirizano watsopano okhudza maiko awiriwa.

Panthawiyo, achinyamata oposa 4000 ndi omwe zinkamveka kuti akudikilira kupita ku Israel.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
1 Comment
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
Moses zgambo
Moses zgambo
1 month ago

Atichedwesa kwambili timayenela kupita December

Read previous post:
Sale of bonya stopped with immediate effect in Rumphi

Rumphi District Council has asked traders along the lakeshore areas to stop selling small Fish locally known as Bonya for...

Close