Big Joe ang’alula APM ati ndiwokonda za matsenga, sakhululuka ndipo samva za munthu

Yemwe anali mkulu oyendetsa zinthu [Director of Operations] mu chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) a Joe Nyirongo wayankhula mosapsatira mawu za bwana ake akale a Peter Mutharika kuti ndi munthu wokonda zamatsenga, wosakhululuka ndiponso samva za munthu.

A Nyirongo, omwe amatchuka ndi zina loti Big Joe, anena izi pa wailesi ya kanema ya Zodiak lachinayi usiku patangotha mulungu umodzi atawachosa mchipani cha DPP kamba kusowa

Nyirongo: Wadzudzula a APM

mwambo.

Atawafunsa kuti atsimikize zomwe analemba masiku amumbuyomu pa tsamba la mchezo la Facebook kuti DPP ndi chipani cha a sing’anga, a Big Joe sanakane ndipo ananenetsa kuti ananena zoona.

“Bwana Mutharika amanena okha nthawi zambiri tikakumana nawo kuti amaziwa za matsenga ndi za mankhwala. Komanso atolankhani atawafunsa nthawi ina yake ku Page House anawuza ntundu wa a Malawi kuti iwowo palibe angawapange kanthu,” atero a Nyirongo.

Mukuyankhula kwawo a Nyirongo anadzuzulanso a Mutharika kuti ndi mtsogoleri wosakhululuka mukasemphana zochita komanso samva za anthu mukamawawuza mbali yina ya zinthu zomwe agwira iwowo.

Atawafunsa kuti kodi akuyankhula izi panopa chifukwa awachosa, a Nyirongo anati iwowo anayamba kale kuyankhulapo pa zomwe zimachitika mu DPP chifukwa iwowo ndi munthu wokhulupira chilungamo.

“Bwana Mutharika anatiyitanisa tonse ku Page House ku Mangochi ndipo anatisimikira tonse mu NGC kuti iwowo sayima choncho aliyense ali ndi kuthekera akayime ku convention. Kenako chifukwa cha dyera la ena mchipanichi, zinthu zinasintha. Ine ndimafuna chipani chikafike ku convention, tisankhe munthu wachinyamata apitilize. Basi zavuta,” anatero a Nyirongo.

Iwo ananenaponso zokhuza zomwe anafunsidwa ku komiti yokhazikisa mwambo ku Lilongwe kuti nkhani yayikulu inali yofuna kuziwa kuti yomwe anayitanisa nkhumano ndi ndani komanso ndalama zoyendesera nkhumanowo zimachokera kuti.

Mneneri wa DPP a Shadreck Namalomba sanayenkhebe pa nkhani iyi koma matsiku apitawo ananena kuti onse ochosedwa akadali ndi mpata wokapepesa ngati akufuna kubwereranso mu chipani.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Malawian arrested in Bangladesh over K15 billion worth cocaine could face death sentence

Malawi national Towera Soko—who has been arrested in Dakar, Bangladesh, for allegedly being found with 8.3 kilogrammes of cocaine worth...

Close