Boma liwonjezera ndalama ku NEEF kuti alimi ambiri azitenga ngongole

Nduna ya za chuma, a Simplex Chithyola Banda yalonjeza kuti undunawu uwonjezera thumba la ndalama zopita ku ngongole za ulimi kudzera ku bungwe la NEEF kuti alimi ambiri apindule.

A Chithyola ati ndi okhutira ndi momwe bungweli lagawira ngongoleyi nyengo ino komanso kuti anthu akubweza bwino.

Iwo alankhula izi poyamba pa ulendo oyendera alimi omwe anatenga ngongole ya ulimi mdera la ku m’mwera kwa boma la Kasungu.

Nduna ya za ulimi a Sam Kawale omwe ali nawo pa ulendowu ati ulimi ndi phata la chuma cha dziko lino kotero kuti kuthandiza alimi ndi mwayi wa ngongole kungachititse kuti dziko lino lithetse njala komanso umphawi mosavuta.

Mkulu wa bungwe la NEEF a Humphrey Mdyetseni  wati kudzafika tsiku la lero bungweli lapereka ngongole zokwana K92 billion kwa abizinesi komanso  alimi mmadera onse mdziko muno.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Councilors threaten to kick out Zomba mayor, accused of self-centeredness

Some councilors in Zomba have ganged against mayor Davie Maunde accusing him of displaying dictatorial traits and self-aggrandizement. The councilors...

Close