Bungwe la Red Cross Malawi lapeleka Maphunziro apadera kwa atolankhani mu mzinda wa Blantyre

Bungwe la Red Cross Malawi lomwe limaona ndi kuyendetsa za chitetezo ,ufulu ndi thandizo la anthu launikira atolankha pa
zomwe anthu amayenera kutsata mu nthawi ya zipwilikiti za nkhondo kuti iwo pamodzi ndi anthuwa molingana ndi lamulo la m’maiko omwe bungweli likugwiramo ntchito lotchedwa International Humanitarian Law(IHL) m’malamulo ankhondo ,ufulu komanso chitetezo cha anthu kuti atolankhaniwa akhale chotengera uthengawu moyenelera.

Poyankhula pa maphunziro amasiku awiri omwe ayamba lachitatu omwe bungweli likuchititsa ndi atolankhani mu mzinda wa Blantyre ,mtsogoleri wa bungweli a Innocent Majiya ati atonkhani akuyenera kudziwa zambiri potengera kuti iwowa akuyenera kuphunzitsa ena za lamulo la IHL mulumikizana ndi ufulu wawo wa kukhala otetezedwa posatenga nawo mbali pa nkhondo(civilian),mwa zina.

“Lamulo la IHL limasiyanitsa munthu woukira(combatant) ndi wosaukira(civilian),potengera ngati munthuyo wapezeka atanyamula chida cha nkhondo pakati pa chipwilikiti cha nkhondo,izi atolanlhani muzizidziwa bwino kutinso mutithandize kudziwitsa anthu ena ” anatero a Majiya.

Ndipo m’mawu ake mtsogoleri wa bungwe la atolankhàni a mu mzindawu,(Blantyre Press Club), Luke Chimwaza anayamikira bungwe la Red Cross chifukwa chopangitsa maphunzirowa ponena kuti ndiwokodwa kuti bungweli likuzindikira kufunika kolumikizana ndi atolankhani pa ncthito zake.

“Tiyamikire a Red Cross Malawi chifukwa cha maphunzirowa lero , mwatilemekeza ndipo ndife okondwa kuti bungweli limazindikira kufunika kogwira ntchito ndi atolankhani ”

” Ndipo limatikumbukira mu zambiri ,leronso latidalira potitsegula maso kuti tikaphunzira tikhale patsogolo kulimbikitsa anthu powadziwitsa za ufulu ndi chitetezo motsatana ndi lamulo la IHL mu nthawi za nkhondo zodza kaamba kusamvana muzochita” anatero Chimwaza.

Bungwe la Red Cross limagwira ntchito zake m’maiko ochuluka mothandizana ndi nthambi za chitetezo ndi mabungwe ena omwe si a boma ndipo a Red Cross amagwira ntchitozi mosatengera mphamvu za boma komanso mbali ngakhale bungweli limavomelezedwa kudzera mu mkumano wa aphungu ndi adindo ena a boma(parliament).

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
EDITORIAL: Gangata’s Gesture to Suspend Friday’s Demonstration is a Mark of True Statesmanship

In a political climate often clouded by ego, bitterness, and blind partisanship, Democratic Progressive Party (DPP) Central Region Vice-President Alfred...

Close