Chakwera atsindika zakufunika kwa fodya kuti boma lake likwanilitse masomphenya 2063

Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera watsimikizila a Malawi mdziko muno za kufunika kwa fodya ndi cholinga choti dziko lino likwanilitse maloto ake a 2063.

Polankhula pa Vivya Primary School mdela la mfumu yaikulu Njombwa mboma la Kasungu, a Chakwera adati masomphenya a 2063, amalimbikitsa kufunika kochulukitsa ndalama.

“Tikamakamba za masomphenya a Malawi 2063, maso mphenya ochulukitsa chuma chadziko lathu kufikira mulingo oti tizitha kuzidalira tokha, amene amakhala nambala 1 pankhani imeneyi ndi alimi afodya. Mma tauni mwathumu mwachuluka anthu odziwa kuyankhula nkhani zachuma nkumadzitcha akatswiri, koma katswiri weni weni pankhani za chuma ku Malawi kuno ndi mMalawi amene akubweretsa chuma mdziko muno, mMalawi amene akuphusha kuti mubwere Forex mdziko muno, ndipo pa a Malawi amene akubweretsa chuma komanso Forex kwathu kuno nambala 1 ndi mlimi wafodya,” adatero a Chakwera.

A Chakwera adati fodya ndi mbewu yofunika kwabasi mdziko muno ndipo ili ndi tsogolo labwino.

Pakadali pano anthu mboma la Kasungu ndi okondwa ndi mitengo yabwino ya fodya. Mwachitsanzo fodya wabwino wagulitsidwa 3 Dollars 10 sents.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Nyasa Tobacco Buying Company Chairman Buckle commits to fulfill Chakwera’s vision on leaf growers

Chairman of Nyasa Tobacco Buying Company, Konrad Buckle, has expressed commitment to collaborating with President Dr. Lazarus McCarthy Chakwera and...

Close