Chakwera wanenetsa kuti sakutuluka m’boma chaka cha mawa
Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati wina asamanamize anthu m’dziko muno kuti iwo atuluka m’boma chaka cha mawa.
Mtsogoleriyu, poyankhula pa mwambo wokumbukira mtsogoleri wakale wadziko lino Hastings Kamuzu Banda, anati boma lake lipitiliza kupanga zitukuko m’zigawo zonse za dziko lino chifukwa alibe nthawi yolimbana ndi anthu ena.
“Olo anthu okonda ndale za miseche afune kapena asafune, ine sindisiya kupereka 200 miliyoni kwacha ku dera la phungu aliyense,” atero a Chakwera.
Mtsogoleri wa dziko linoyu wati Kamuzu Banda amakhulupilira ndale zoyanjanitsa anthu m’dziko.
Chakwera wayamikiranso banja la a Banda povomera kuti mwambo wokumbukira mtsogoleri wakale wadziko linoyu, udzichitikira muzigawo zonse za dziko lino.
Follow and Subscribe Nyasa TV :