Chenjerani! Loreal Dark and Lovely ndiwoyipa, ali ndi chiopsezo pa moyo wanu, boma latero
Bungwe loona za chilungamo pamalonda la CFTC lati lalandila uthenga kuchoka ku kampani ya Loreal South Africa kuti yayamba kuitanitsa mankhwala otsukira tsitsi a Loreal Dark and Lovely Anti Breakage Kit komanso Mosture Plus Kit (Regular and Super) kamba koti ali ndi chiopsezo kuumoyo wa athu.
Mneneri kubungwe la CFTC an Innocent Herema wati kampaniyi yawauza kuti mu mankhwalawa mukumapezeka tizilombo (Bacteria) tomwe tikumakhudza khungu la m’mutu mwa munthu komanso kusokoneza chitetezo chamthupi lamunthuyo.
A Helema ati uthenga omwe ali nawo waonetsa kuti mankhwalawa anakonzedwa m’mwezi wa April mdziko la South Africa.
Komabe bungwe la CFTC lati silinachite kafukufuku pofuna kupeza ngati mtundu wamankhwala otsukila tsitsiwa ukupezeka pamisika yam’dziko lino, ndipo a Helema apempha anthu omwe akugulitsa mankhwalawa kuti akabweze komanso a Malawi kuti asiye kugwiritsa ntchito mankhwalawa.