Chimbudzi cha K15.9 million ku Rumphi chagwa
Chimbudzi cha ndalama zokwana K15.9 million chomwe khonsolo ya Rumphi inamanga pa nyumba yodikilira amayi apakati pa chipatala cha Rumphi chagwa masanawa.
Wapampando wa komiti ya zaumoyo pachipatalachi a Manase Mhango wati akukaikira kuti chimbudzichi chagwa kamba koti sichinamangidwe molimba.
A Mhango ati pakadali pano adziwisa kale DC wabomali za nkhaniyi ndipo ati palibe wavulala ndi ngoziyi.
Chimbudzichi chagwa patangodusa chaka chimodzi kuchokela pomwe khonsolo yabomali inachipeleka kwa amayi pachipatalachi kuti azichigwiritsa ntchito.
Follow and Subscribe Nyasa TV :