Chithyola akhazikisa ntchito yopereka ndalama kwa anthu ovutika okhala m’matauni: Anthu ayamba kulandira

Nduna yoona zachuma Simplex Chithyola- Banda watsindika kuti anthu amene amakhala m’matauni nawonso amakumana ndi umphawi wa dzaoneni.

Nduma ya za chuma a Chithyola-Banda

A Chithyola-Banda anena izi m’boma la Zomba pa mwambo okhazikitsa ndondomeko ya mtukula pakhomo wa m’mizinda ya Zomba, Blantyre, Lilongwe komanso Mzuzu.

Malingana ndi ndunayi,ndi mtukula pakhomowu, umene ukuthandizidwa ndi a World Bank, mabanja okwana 105 000 ndi amene apindule kwa miyezi itatu ndipo aliyense azilandira ndalama zokwana K150 000 kudzera pa foni zawo.

Zalowa? Ena mwa olandira chithandizochi akuwona ngati ndalama zalowa

“Dziko lino likhoza kupita patsogolo ndi chitukuko ngati anthu akumidzi ndi ntauni akhale odzidalira pa chuma,” adatero a Chithyola-Banda.

Nduna yowona kusasiyana pakati pa amuna ndi akazi komanso chitukuko cha kumadera a Jean Sendeza,alangiza anthu amene apindule ndi ndondomekoyi kuti ndalama za mtukula pakhomo zizitukuladi makomo osati kubweretsa chipasupasu m’mabanja.

Jean Sendeza

Iwo anati: “Ndalamayinso sikuti mungogulira zakudya ndi kutha, koma muyigawe ndikuchita ma bizinesi ichulukane kuti patsogolo mudzakhale odzidalira panokha.”

Mfumu ya mzinda wa Zomba a Davie Maunde poyikirapo ndemanga, anati aonetsetsa kuti anthu amene akuyenera kulandira ndalamayo ndi omwe akupinduladi ndi thandizoli.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
As the cost-of-living soars, govt reduces budget allocation to refugees dept from K900m to K704m

Coalition of Civil Society Organizations advocating for the welfare of refugees and asylum seekers has bemoaned the reduction of the...

Close