Moto wabuka ku UDF! Magavanala a chigawo chapakati aphwasula komiti pawokha

Magavanala a m’ma boma a chigawo chapakati mchipani cha UDF athetsa komiti yawo yayikulu mchigawochi ati chifukwa mamembala amakakamila ma udindo.

Polankhula m’malo mwa magavanalawa pa msonkhano wawo ku Lilongwe masanawa, a Saidi Bauti anati ndiwokhumudwa ndi mene chipanichi chimasankhira adindo oyendetsa chipanichi mchigawochi.

Iwo ati akhala akulembera akuluakulu achipanichi zokhudza nkhawa zawo kuyambira 2009 koma palibe chomwe akuluakuluwo achita pa nkhaniyi.

Atsogoleriwa asankha komiti yongogwirizira komanso awuuza chipanichi kuti chichititse chisankho cha adindo a chigawochi pasanathe masiku 21.

Mneneri wa UDF a Yusufu Mwawa wati analandira madando a anthuwa koma alibe mphamvu zothetsa komiti ya chigawo malinga ndi malamulo achipanichi.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Chithyola akhazikisa ntchito yopereka ndalama kwa anthu ovutika okhala m’matauni: Anthu ayamba kulandira

Nduna yoona zachuma Simplex Chithyola- Banda watsindika kuti anthu amene amakhala m'matauni nawonso amakumana ndi umphawi wa dzaoneni. A Chithyola-Banda...

Close