DPP ikufuna boma lilole kuti anthu opanda chiphatso cha unzika azavote nawo chaka cha mawa

Mtsogoleri wa aphungu achipani cha DPP mnyumba yamalamulo a Mary Navicha wati aphungu achipanichi apempha boma ndi bungwe la MEC kuti alole anthu ngakhale alibe chiphatso cha unzika koma anakwanitsa zaka zoponya voti kuti azawalore kuponya voti pachisankho cha chaka chammawa.

A Navicha ati ganizoli ladza kutsatira kulephera kwa bungwe loona zakalembera wa unzika kulemba anthu mkaundula wa unzika ponena kuti madera ambiri maka kuchigawo chakummwera anthu sanalembetse.

 

Iwo amalankhula izi pamsonkhano wa olemba nkhani omwe akuchititsa ku Lilongwe. Iwo pamodzi ndi aphungu ena achipanichi ati akhale akukumana ndi akuluakulu ku nthambi zoyenera pankhaniyi.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Bungwe la United Nations liyamikila Chakwera kamba kopititsa patsogolo ntchito zotukula amai mdziko muno

Bungwe la United Nations (UN) layamikila mtsogogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera kamba koonetsa chidwi pa ntchito yotukula...

Close