Katsonga ang’alula: Ati Malawi sikutukuka chifukwa timasankha atsogoleri opanda ndalama akamalowa m’boma

Nduna yakale yazamalonda a Mark Katsonga Phiri yati dziko lino likukanika kutukuka kamba koti anthu amavotera adindo omwe amalowa m’boma alibe ndalama komanso luntha lopanga ndalama koma kusakaza misonkho ya Malawi.

Katsonga: PPM president now MP

Iwo alankhula izi pamwambo okhazikitsa mwala wamaziko pasukulu ya sekondale ya Ligowe pomwe pakhale malo ophunzilira komputa zomwe ati zithandizira kukweza maphunziro m’boma la Neno.

 

Iwo atinso boma limakangalika kugula zinthu zosathandiza monga nsalu ndi matisheti achipani, zomwe iwo amatsutsa ali nduna ndipo zinawachosetsa paundunawu.

 

Padakali pano, iwo ayamikila bungwe la Macra pantchito yomanga malo ophunzilira luso lamakonoli.

 

Mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi a Everlisto Chamasowa wati malowa athandiza pomwe boma likulimbikitsa ntchito yogwiritsa ntchito zipangizo zamakono pophunzira.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter