Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe iyamba ntchito yosamutsa mtaya
Malipoti omwe akungotipeza kumene akusonyeza kuti Khonsolo la Mzinda wa Lilongwe layambapo ntchito yosamutsa mtaya wa zinyalala kuchokera ku dela 38 mumzindawu.
Mfumu yamzinda wa Lilongwe Khansala Richard Banda ndi imene yanena izi lero pa nsonkhani wa atolankhani mumzinda wa Lilongwe.
A Banda anati Khonsolo yalemba kale ntchito anthu yowunika zonse zokhudza ntchito yosamutsa mtayayi.

Iwo adati Khonsolo yapeza kale malo omwe pakakhale mtaya watsopanowu.
Anthu a muzinda wa Lilongwe akhala akudandaula za mtaya umenewu omwe wakhala ukubweretsa chiopsezo ku miyoyo yawo.
Follow and Subscribe Nyasa TV :