Tamia Ja amangidwa poganiziridwa kuti anazembeyesa K8 miliyoni ya mwini
Apolisi munzinda wa Lilongwe amanga mmodzi mwa anthu odziwika bwino pamasamba amchezo Hannah Jabes, yemwe amadziwika bwino ndi dzina la Tamia Ja, kamba kankhani yogwirizana ndi kuba.
Malingana ndi a polisi, masiku angapo apitawo analandira dandaulo kuchokera kwa mkulu wina wochita malonda yemwe anati Tamia Ja anazambayitsa ndalama zokwana 8 million kwacha zitaikidwa molakwika mu akaunti yake.
Poyankhula mneneri wa polisi ya Lingadzi Cassim Manda wati Tamia Ja poyamba anauza munthu yemwe anatumiza molakwika kuti walandiradi ndalamazi ndipo abweza koma panthawiyo anali paulendo wopita mdziko la South Africa.
Manda anawonjezera kunena kuti kuchokera nthawi imeneyo Tamia Ja anayamba zozembazemba kuti abweze ndalamazi mpakana pakadali pano wamangidwa ndi apolisi.