Kamlepo ayambitsa phokoso ku Parliament atadzudzula boma kuti sililabadira anthu aku mpoto

Ku nyumba ya malamulo kunabuka chipwirikiti masanawa, zomwe zidapangitsa kuti Kamlepo Kalua, phungu wa dera la ku mmawa m’boma la Rumphi komanso Christopher Manja phungu wa dera la ku m’mwera kwa boma la Salima atulusidwe mnyumbayi.

Kamlepo Kalua

Kalua anadzudzula boma lotsogozedwa ndi Tonse kuti silisamala chigawo chakumpoto pa ntchito zachitukuko ponena kuti boma lapereka ndalama zokwana 18 biliyoni kwacha pa ntchito yokonza misewu m’madera ena.

Koma panthawiyi, phungu wa Salima South Christopher Manja anayima kuti alankhulepo pa nkhaniyi zomwe zinapangisa kuti awiriwa asemphane chichewa mpaka kufika kuuzana kuti “akamenyane panja”.

Wachiwiri kwa sipikala ku Nyumba ya Malamulo, Madalitso Kazombo, adalimbikitsa aphungu kuti apewe mawu omwe angadzetse kugawanikana pakati pa a Malawi.

Pambuyo pake, potengera lamulo 105 la nyumba ya malamulo, Kazombo adatulusa Kalua ndi Manja ndipo walamula kuti awiriwa asapezeke ku nyumbayi kwa masiku asanu.

Poyankhapo, Richard Chimwendo Banda mtsogoleri wa zipani za boma wati boma limapereka chitukuko mofanana ndipo silitengera komwe anthu akuchokera

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Jenda-Edingeni- Mzimba Boma will be completed, Chakwera assures people of Mzimba

Malawi leader President Lazarus Chakwera has assured people of Mzimba his government commitment to complete Jenda - Edingeni Road. Speaking...

Close