‘Kulira kwake ndiye nkumatani abale?’ Chipani cha UTM chalira kumwalira kwa Lucius Banda

Chipani cha UTM chati imfa ya Soldier Lucius Banda mnjowawa kwambiri maka pomwe chipanichi chikulirabe mtsogoleri wawo a Saulos Chilima.
Lucius Banda anali mkulu okopa (Campaign Director) anthu mchipani cha UTM.
Akumananso
Mneneri wa UTM a Felix Njawala wati ngati chipani sakudziwa kuti nkumatanino ndi momwe imfa yatengera akuluakulu ake motsogozana.
Afotokoza a Njawala: “Pomwe a Chilima ankachokera ku South Korea posachedwa, adadzera ku South Africa kukamuona Lucius Banda.
“Akuluakulu a chipani angapo akhalanso akukamuona. Sitinaganize kuti zithera chonchi. Kulira kwake ndiye nkumatani abale?”.
Mu mauthenga awo omwe awaponya ma masamba a mchezo osiyana siyana, oyimba ambiri ati imfa ya Soldier ndi yopweteka kwambiri potengera kuti oyimbayu anali ndi mtima othandiza oyimba amzake komanso ochezeka.
“Chonena chikundisowa. Imfa iyiyi ndi yopweteka kwambiri,” watero mtsogoleri wa gulu loyimba la Black Missionaries Anjiru Fumulani.
Oyimba wina Wendy Harawa naye wadandaula motere: “Chonena ndilibe. Ambuye timvereni chisoni.”
Oyimba ndi amalawi ena ambiri akupitiliza kupeleka mauthenga awo okhuza imfayi. Lucius Banda wamwalira Ali ndi Zaka 54.
Naye oyimba Steve Muliya wati Lucius Banda anali msanamila ya zoyimbayimba muno mmalawi. Ambiri a oyimbawa agawa zinthu zomwe anajambulitsa limodzi ndi a Lucius Banda.
Mukulira kwawo, bungwe la oyimba m’dziko muno la Musicians Union of Malawi – MUM lati Lucious Banda anali munthu wachikondi komanso odzichepetsa.
Mtsogoleri wabungweli Vita Chirwa wanena izi kutsatira infa ya Banda lero mdziko la South Africa.
“Mutha kuwona kuti anathandiza oyimba ochuluka mdziko muno zomwe zikuphelezera za chikondi chomwe anali nacho pa anzake,” watero Chirwa.
Chirwa watinso anakambilana ndondomeko zosiyanasiyana kuti apange ndicholinga chofuna kutukula oyimba m’dziko muno. “Nditangosankhidwa pa udindowu, anandiyimbila phone mkundiuza kuti agwira nane ntchito, ndiye pano mkumanva zamaliro, ndipanga bwanji tsopano,” watero Chirwa yemwe amanveka wachisoni kwambiri.
Banda wamwalira ali mlangizi wa mtsogoleri wa dziko lino pa nkhani za luso komanso achinyamata.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Parliament meets Mangochi resort hotels and lodges to induce them to SRWB water supply

The Parliamentary Committee of Natural Resources & Climate Change has invited owners of major resort hotels and lodges in Mangochi...

Close