Kwavuta ku Balaka! Nzika zakangalama kuti sizichoka pa ofesi ya Escom mpaka akonze transformer

Nzika zokhudzidwa ndikuvuta kwa magetsi mdera la Majiga 2 mtawuni ya Balaka zayamba mbindikiro pa ofesi za ESCOM pofuna kukakamiza bungweli kuti liwakonzere transformer imene idaonongeka.

Sabata yatha, gululi linapeleka kalata ya madandaulo awo ku ofesi ya bungweli kuti ipeleke mayankho ku nkhawa zawo.

M’modzi mwa anthuwa, a Pretorius Halidi wati kuzima kwa magetsi kwa mwezi tsopano kwakhudza ntchito za malonda komanso umoyo wa anthu ambiri kaamba koti amadalira magetsi tsiku ndi tsiku.

Iwo ati akhala akuchita m’bindikirowu kufikira atapeza mayankho omveka. Mneneri wa ESCOM a Kitty Chingota adati akudziwa za vuto la transformer ya m’derali ndipo achitapo kanthu.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Apostle Nyirongo vows that for the world to prosper, we need ‘righteous leaders’

Apostle Hellings Nyirongo, founder for Christ Fellowship Church for All Nations (CFCAN), says for the world to prosper, it needs...

Close