Kwavuta ku MCP pomwe akuluakulu ena mchipanichi adzudzula a Mkaka paganizo lakayendesedwe ka Convention
Apampando mzigawo zinayi za chipani cha MCP alembera mlembi wamkulu mchipanichi a Elsenhower Mkaka kuwawuza kuti sakugwirizana ndi zomwe anena kuti ofesi yawo idzayamba yaunika kaye anthu olowa mchipanichi asadavomerezedwe.
Anayiwa ndi a Zebron Chilondola, a Joseph Chavula, a Peter Simbi komanso a Augustine Chidzanja.
Akuluakuluwa ati akutsutsana ndi ganizo lomwe linapangidwalo ndipo ati ngati akufuna zimenezo, a Mkaka nawonso aunikire bwino momwe anapezera udindo mchipanichi.
Iwo atinso ngati pali kusitha kwina kuli konse, malamulo achipanichi asinthidwenso.
Koma a Mkaka ati owona za malamulo mchipanichi adavomereza maganizo awo ndipo ngati ena ali ndi madandaulo akatule ku ofesi yovomerezeka.
Posachedwapa, MCP idalengezanso kuti onse ofuna kupikisana nawo ku mkumano wawo waukulu mu August akhale kuti ndi membala kwa zaka zosachepera ziwiri komanso kuti adakhalako ndi udindo mchipanichi.
Follow and Subscribe Nyasa TV :