Mabungwe oti siaboma pafupifupi 565 akhoza kuimitsidwa kugwira ntchito mdziko muno: Chachitika ndi chani?
Pali chiopsezo chenicheni choti mabungwe oti siaboma pafupifupi 565akhoza kuimitsidwa kugwira ntchito komanso kupatsidwa chindapusa ngati satsatira lamulo la NGO ACT.

Lamuloli limaonetsetsa kuti mabungwe omwe adalembetsedwa adzipereka lipoti ku boma kudzera ku bungwe loona za mmene mabungwe omwe siaboma akugwirira ntchito la Non Governmental Organizations Regulatory Authority (NGORA).
Izi amayenera kuchita pofika pa 30 June chaka chilichonse kuti adzitha kulandira chiphaso chogwirira ntchito chatsopano.
Koma mkulu wa bungwe la NGORA a Edward Chileka Banda, pa mabungwe 1045 omwe adalembetsedwa, mabungwe 480 okha ndi omwe pakadali pano akwanitsa kupereka lipoti ku boma ndikupeza ziphaso zogwirira ntchito zatsopano.
Komabe, iwo ati aika chidwi pochita zokambirana ndi mabungwe omwe sadapereke malipotiwa kuti aonetsetse kuti atsatira lamulo.
Woyankhulapo pa nkhani za ulamuliro wabwino a Victor Chipofya wati zomwe akuchita mabungwewa ndizopereka mafunso ngati amachita zinthu zawo poyera.
“Pali mabungwe ena omwe cholinga chawo kwenikweni ndi kupeza phindu pa ndalama zomwe amalandira kuchoka kwa owathandiza mwina ndi chifukwa chake akulephera kupereka tsatanetsatane wa zomwe akhala akuchita kuti alandirenso chiphaso chogwirira ntchito,” iwo atero.
Follow and Subscribe Nyasa TV :