Malawi ndi Zambia ikuthetsa miseche kudzera mwa DJ Kachamba ndi General Kanene
Wabweranso DJ Kachamba, pano nde wabwera ndi General Kanene pomwe oyimba awiriwa anyamula mbendera ya Malawi ndi Zambia polimbana ndi mchitidwe wa mabodza mu nyimbo yatsopano Miseche.
Mu nyimboyi, awiriwa akuti mchitidwe wamiseche ndi umthira kuwiri ukupititsa pansi chitukuko cha maiko oyandikanawa.
Ngakhale izi zilo chomwechi, awiriwa akupempha mchitidwe oti anthu azimasukirana pakakhala kufunika kopereka chidzudzulo ‘osati kumwerana mowa kuti palalatidwe’.
Mwachitsanso DJ Kachamba wati mchitidwe wamiseche ukupangitsa kuti anthu ena adzikhala mopanda mtendere.
‘’Anthu ali pano, ndiovuta. Ngigule munda, ndzilima. Ati ndine okhwima. Ndigule galimoto nde mavuto onenedwa. Bola ndingolowera.’’ Ikutero nyimboyo.
Ndipo Kanene naye, wati ku Zambia anthu omwe sakondwera ena akamachita bwino aliko.
Komai ye wati, anthu omwe amanenedwa azilimbikirabe ndipo asafooke.
Nyimboyi yajambulidwa ku Favor Records ndi Elia Phiri.
Iye anati munyengo yonga iyiyi, anthu akuyenera kukhala ndi chidwi poti ena anangobadwa ndi mchitidwe obwezera anzawo mbuyo.
Pakadali pano, Kachamba wati apitiriza kutulutsa nyimbo zokamba mavuto omwe anthu amakumana nawo popereka njira zomwe angathanirane ndi mavutowa.
DJ Kachamba yemwe dzina lake ndi Simeone Masanjala, m’bale wa oyimba odziwika kuyambira kale Daniel Kachamba ndipo akukhala ku South Africa anatulutsa abamu ya nyimbo 11 yotchedwa Alipobe chaka chatha momwe munali nyimbo monga Chauta ndinso Maliro.
Follow and Subscribe Nyasa TV :
We are proud of you