Mtima wokonda zakunja ukulowetsa pansi chuma chathu – Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera wati mtima wokonda kuyitanitsa katundu ku mayiko akunja womwe Amalawi ambiri ali nawo ndi umene ukulowetsa pansi chuma cha dziko lino.

Chakwera ananena izi Lachitatu pamene amatsegulira chiwonetsero cha malonda mu mzinda wa Blantyre. Chiwonetsero cha malonda chimakonzedwa chaka chilichonse ndi bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI).

Mmau awo potsegulira chiwonetsero cha chaka chino, Pulezidenti Chakwera anadandaula ndi mchitidwe wogula zinthu za kunja popanda kugulitsa zinthu zadziko lino kunja mokwanira, zomwe akuti zikulowetsa pansi chuma cha dziko.

“Ndiye aliyense wopanga bizinesi akudziwa kale kuti ukamagula kapena kuoda katundu ochuruka kwambiri kuposa amene ukugulitsa, geni ndiye kuti ikulowa pansi. Ndiye tikati titenge dziko la Malawi ngati geni, ndiye kuti geni yathu yakhala ikulowa pansi nthawi yayitali chifukwa chogula katundu ochuluka kwambiri kuposa amene tikugulitsa. Mwa chitsanzo, mu March chaka chatha, zogula kunja zinachuluka kopusa zogulitsa kunja ndi mulingo okwana 177.7 million dollars, pamene mwezi omwewo chaka chino mulingowo unakweranso nkufika 194.4 million dollars, kusonyeza kuti vutoli lidakali lalikulu,” anatero mtsogoleriyu.

Chakwera anadzudzulanso mchitidwe wotapa ndalama zakunja pokagula katundu wakunja popanda kubwezeretsa ndalamaza zakunjazo pogulitsa katundu mayiko akunja.

Iye anati izi ndizimene boma lake lakhala likukonza kuti zisinthe.

“Mbali imodzi yomwe tikuonetsetsa kusintha izi ndi kuchulukitsa zaulimi zomwe timagulitsa kudzera minda ikuluikulu ija ya ma Mega Farm komanso kulimbikitsa ulimi wanthilira, chifukwa chinthu chimodzi chomwe chakhala chikulowetsa pansi malonda aulimi ndi kukakamila ulimi odikira mvula komanso ulimi wakhasu, omwe suupanganika chifukwa cha kusintha kwa nyengo komanso omwe umangokolola chakudya chochepa chokha. Ndichifukwa chake sabata lathali, ndimakhazikitsa pulogramu yowathandiza alimi kupeza matrakitale, komanso ndichifukwa tikukhazikitsa masikimu aulimi wanthirira mzigawo zonse,” iwo anatero.

Pulezidenti Chakwera anati cholinga chaulimi wabizinesi ndi kuchulukitsa malonda amene dziko lino limagulitsa kunja kuti alimi azipindula.

Iye anati ndi bodza la mkunkhuniza kuti ulimi siukuyenda ku Malawi, popereka chitsanzo cha alimi afodya amene chaka chino akusimba lokoma ku msika chifukwa boma laek likuwamenyera nkhondo yogulitsa fodya wawo pamtengo wabwino kuposa kale.

“Ndipo inu amabizinesi amene mukugula fodya ameneyu ndikuthokozeni polimbikitsa bizinesi yaulimi kuti ipitilire kukhala yotentha, komanso ndithokoze eni ake alimiwo pogwira ntchito molimbikira komanso potsatira uphungu wamalimidwe amakono.

“Kwangotsalano kuti zomwe zikuchitika ku bizinesi ya ulimi wafodya zichulukitsidwenso ku bizinesi ya ulimi wambeu zina zomwe tikufuna tikuthandizeni kugulitsa mayiko ena mwakathithi. Ubwino wake izi zayamba kale kuchitika komanso zotsatira zake zayamba kale kuoneka. Koma kuti zimenezi zifike posintha chuma chadziko, ife aboma ndi inu a Private Sector tikuyenera tigwirane manja kuti tithamangatse zinthuzi limodzi. Ndipo ife aboma tili okonzeka kutukula ma bizinesi ndikuwapatsa kuthekera ogulitsa katundu wawo mayiko ena. Ndipo zotukula mabizinesi ndikupeza misika yokunja sitikupangira mabizinesi aulimi okha, chifukwa masomphenya ochulikitsa chuma chobwera mdziko muno sangakwaniritsidwe ndi ulimi okha,” anatsindika chonchi a Chakwera.

Pomaliza, Chakwera anapemba amalonda kuti agwiritse ntchito mwayi womwe dziko lino likupereka kudzera mkutsegulidwa kwa misika kudzera mu African Continental Free Trade Area (AfCFTA), (COMESA) ndi Southern African Development Community (SADC) komanso ku dziko la China.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
UK charity organization, Against All Odds Still Standing, empowers needy women, students

A (UK) based charity organization called Against All Odds Still Standing (AOS) has re-embarked on a mission to empower women...

Close