Ngkhale CDF yakwezedwa kuchoka pa K100m kufika pa K200m, aphungu akufuna ikwelenso ifike pa K1 biliyoni

Aphungu akunyumba yamalamulo ati ndipofunika ndalama zamuthumba lachitukuko la Constituency Development Fund (CDF) zidzafike pafupifupi K1 billion kuti aphunguwa adzikwanitsa kupanga zitukuko zogwirika zomwe anthu am’madera awo amafuna.

Wapampando wakomiti yanyumba yamalamulo yazosamalira anthu Sarvel Kafwafwa ndiyemwe wanena izi poyerekeza kuti maiko monga Zambia ndi Kenya thumbali lili ndi ndalama zochuluka mwakuti aphungu savutika kumapempha zitukuko monga zipinda zophunzilira mnyumba yamalamulo.

Izi zikudza pamene anthu mdziko muno akhala akupereka maganizo osiyana kutsatira kukwezedwa kwa ndalama zamuthumbali mundondomeko yachaka cha 2024/25 kuchoka pa K100 million kufika pa K200 million.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Zandikwana! Enock Chihana akuti amanga yekha chiliza cha abambo ake: Boma latinamiza mokwanira

Mtsogoleri wa Aford a Enock Chihana ati pa 6 April chaka chino akhala akukhazikitsq ntchito yomanga chiliza cha malemu Chakufwa...

Close