Zandikwana! Enock Chihana akuti amanga yekha chiliza cha abambo ake: Boma latinamiza mokwanira
Mtsogoleri wa Aford a Enock Chihana ati pa 6 April chaka chino akhala akukhazikitsq ntchito yomanga chiliza cha malemu Chakufwa Chihana omwe anali bambo ake. Iwo ati akulu akulu ena aku mabungwe monga a United Nations komanso mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr Bakili Muluzi awalonjeza kuti akayamba ntchito yomanga chilizachi adzawathandiza.
Iwo alankhula izi pamwambo omwe achipani cha Aford anakonza olambula kumanda a malemu Chakufwa Chihana mu mzinda wa Mzuzu.
A Chihana ati mbuyomu akubanja samachita kanthu pankhani ya chiliza cha bambo awo kamba koti boma linalonjeza kuti limanga chiliza cha malemu Chakufwa Chihana.
“Ine ngati mwana oyamba wa a Chakufwa Chihana ndikupepesa akubanja onse kamba koti papita zaka 18 chiliza cholongosoka cha bambo awo chisanamangidwe”anatero a Chihana.