Ntchito yokumba mjigo m’boma la Nkhata Bay yayambika

Boma ndithandizo lochokera ku Global Fund likukumba mijigo mmadera osiyanasiyana a mmdziko muno pofuna kuchepetsa matenda omwe amabwera kamba ka madzi.

Polankhula pomwe anayendera imodzi mwa ntchito yomwe ikuchitika ku Biya m’boma la Nkhata bay, wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo Mayi Halima Daud anati ndi cholinga cha boma kufuna kuti anthu a mdziko muno akhale ndi madzi abwino pofuna kuteteza miyoyo yawo ku matenda.

“Ndine okondwa ndi okhutira powona kuti ntchito yokumba chitsime yayamba bwino pomwe midzi yambiri ikhale ikugwiritsa ntchito madzi a ukhondo posachedwa,” anatero a Daud.

A Daud anawonjezera kuti zitsime zambiri zikufunika mdziko muno ndipo apempha akufuna kwabwino kuti alithandize boma kupereka madzi a ukhondo ku madera komwe anthu akukhala.

Phungu wa delali, Mayi Chrissy Kanyasho wayamikira boma pobwera ndi chitukuko cha madzi mdera lake.

“Mjigo umenewu uthandiza kwambiri anthu ozungulira midzi imeneyi pokhala ndi madzi a ukhondo,” anatero.

Mfumu Peter Chavula ya mderali inali ndi chimwemwe chachikulu ndipo inayamikira boma kamba ka thandizoli.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
NBM splashes prizes in “Popanda Chifukwa” Promo

Bank of the nation, National Bank of Malawi (NBM) plc has splashed various prizes to winners of the first monthly...

Close