Nthambi ya za Nyengo alosera mvula yochuluka mnyengo ya mchaka chino ndi cha mawa
Nthambi yowona za Nyengo ndi kusintha kwa Nyengo mdziko muno yalosera nyengo la dzinja mchaka chino ndi cha mawa (2024/2025) kuti kukhala mvula yochuluka poyelekeza ndi dzinja lapitali.
Mkulu woyang’anira nthambiyi, a Lucy Mtilatila awuza atolankhani mu mzinda wa Lilongwe la chisanu kuti ngakhale zili chomwechi, Pali chiyembekezo chakuti mwezi wa November utha kukhala ndi mvula yochepa m’madera ochuluka zomwe zingakhuze chiyambi Cha mvula yodzalira.
“Chingakhale mvula ikhoza kuvutilapo pa chiyambi pake, ulosi wa dzinjali ukusonyeza kuti mvulayi ikayamba idzakhazikika ndipo pali chiyembekezo cha dzinja labwino ndi la mvula yochuluka,” atero a Mtilatila.
Iwo awonjezera kuti pali chiyembekezo kuti mvulayi ikhoza kuthandizila kuti zokolora zichite bwino komanso komanso kuti madzi akhale akupezeka mosavuta.
A Mtilatila ati komabe ziopsyezo monga kusefukira kwa madzi kukhoza kukhuzanso zokolora, Katundu, zipangizo zosiyanasiya ngakhalenso miyoyo.
Kuphatikiza apo ulosi-wu ukusonyezanso kuti dzinja la chaka chino lithandiza kuti madzi akhalebe okwera mu nyanja ya Malawi.
“October mpaka December chaka chino madera ambiri m’dziko muno akuyembekezereka kulandira mvula ya mlingo okhazikika kapena kuchepera apo. Madera ena a chigawo cha pakati ndi mphepete mwa nyanja ku mpoto akuyembekezereka kulandira mvula ya mlingo okhazikika kapena kuposa apo,” a Mtilatila anafotokoza.
Kuonjezela apoJanuary mpaka March, 2025 mvula yoposera mlingo okhazikika ikuyembekezela kugwa mu nyengo-yi m’madera ambiri a mu dziko muno.
“Dzinja la 2024 mpaka 2025, likhuzidwa ndi La Nina ochepa mphamvu. Nyengoyi imadzetsa mvula yochuluka ku mwera kwa Africa kuphatikizapo ku mwera kwa Malawi,” a Mtilatila anatelo.