Phungu wa DPP ku Mangochi wati awonesesa kuti Chakwera apitilize kuyendesa Malawi
Phungu wa chipani cha Democratic Progressive Party wa dera la kumpoto m’boma la Mangochi, Benedicto Chambo, wati agwira ntchito yothandiza kuti mu 2025, President Lazarus Chakwera apitirize kulamula dziko lino.
Phunguyu lero adali nawo pa msonkhano wa chipani cha Malawi Congress umene unachitikira pa bwalo la masewero la Dzenza, ku Area 25 m’boma la Lilongwe.
Mlendo wolemekezeka pa msonkhanowu adali nduna ya maboma aang’ono a Richard Chimwendo Banda yemwenso ndi mkulu wa achinyamata mu chipani cha MCP.